Ndipo Abrahamu analawira m'mamawa, natenga mkate ndi thumba la madzi, nampatsa Hagara, naika paphewa pake, ndi mwana, namchotsa iye: ndipo iye anamuka, nasocherera m'chipululu cha Beereseba.
Genesis 26:23 - Buku Lopatulika Ndipo anachoka kumeneko nakwera kunka ku Beereseba. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anachoka kumeneko nakwera kunka ku Beereseba. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Patapita nthaŵi, Isaki adachoka napita ku Beereseba. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Isake anachoka ku malo kuja kupita ku Beeriseba. |
Ndipo Abrahamu analawira m'mamawa, natenga mkate ndi thumba la madzi, nampatsa Hagara, naika paphewa pake, ndi mwana, namchotsa iye: ndipo iye anamuka, nasocherera m'chipululu cha Beereseba.
Ndipo Abrahamu anabwera kwa anyamata ake, ndipo anauka nayenda pamodzi kumuka ku Beereseba; ndipo anakhala Abrahamu pa Beereseba.
Ndipo Israele anamuka ulendo wake ndi zonse anali nazo, nafika ku Beereseba, napereka nsembe kwa Mulungu wa Isaki atate wake.
koma musamafuna Betele, kapena kumalowa mu Giligala; musamapita ku Beereseba; pakuti Giligala adzalowadi m'ndende, ndi Betele adzasanduka chabe.
Pamenepo anatuluka ana onse a Israele, nuunjikana msonkhano kwa Yehova ku Mizipa ngati munthu mmodzi, kuyambira ku Dani mpaka Beereseba ndi dziko la Giliyadi lomwe.