Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 26:22 - Buku Lopatulika

22 Ndipo anachoka kumeneko nakumba chitsime china; koma sanakangane nacho chimenecho; ndipo anatcha dzina lake Rehoboti; ndipo anati, Chifukwa kuti tsopano Yehova anatipatsa ife malo, ndipo tidzabalana m'dziko muno.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Ndipo anachoka kumeneko nakumba chitsime china; koma sanakangane nacho chimenecho; ndipo anatcha dzina lake Rehoboti; ndipo anati, Chifukwa kuti tsopano Yehova anatipatsa ife malo, ndipo tidzabalana m'dziko muno.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Adachoka kumeneko, nakakumba chitsime china. Pa chimenechi panalibe mkangano, motero adachitcha Ufulu. Adati, “Tsopano Chauta watipatsa ufulu m'dziko, ndipo tidzalemera kuno.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Anachokapo pamenepo nakakumba china. Koma apa sanakanganiranenso ndi munthu. Iye anachitcha Kutakasuka, nati, “Tsopano Yehova watipatsa ife malo otakasukirako ndipo tilemera muno.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 26:22
11 Mawu Ofanana  

Ndipo ndikubalitsa iwe ndithu, ndipo ndidzakuyesa iwe mitundu, ndipo mafumu adzatuluka mwa iwe.


Ndipo anakumbanso chitsime china, ndipo anakangana nachonso; natcha dzina lake Sitina.


Mulungu Wamphamvuyonse akudalitse iwe, akubalitse iwe, akuchulukitse iwe, kuti ukhale khamu la anthu:


Ndipo dzina la wachiwiri anamutcha Efuremu: chifukwa Mulungu anandibalitsa ine m'dziko la kusauka kwanga.


M'mene ndinasautsika ndinaitanira pa Yehova; anandiyankha nandiika motakasuka Yehova.


Ndidzathamangira njira ya malamulo anu, mutakulitsa mtima wanga.


Ananditulutsanso andifikitse motakasuka; anandilanditsa, pakuti anakondwera ndi ine.


Pakufuula ine mundiyankhe, Mulungu wa chilungamo changa; pondichepera mwandikulitsira malo. Ndichitireni chifundo, imvani pemphero langa.


Ana a Israele ndipo anaswana, nabalana, nachuluka, nakhala nazo mphamvu zazikulu; ndipo dziko linadzala nao.


Kuza malo a hema wako, afunyulule zinsalu za mokhalamo iwe; usaleke, tanimphitsa zingwe zako, limbitsa zikhomo zako.


Pakuti iwe udzafalikira ponse padzanja lamanja ndi lamanzere, ndipo mbeu yako idzalandira amitundu cholowa chao, ndi kukhalitsa anthu m'mabwinja.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa