Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 21:14 - Buku Lopatulika

14 Ndipo Abrahamu analawira m'mamawa, natenga mkate ndi thumba la madzi, nampatsa Hagara, naika paphewa pake, ndi mwana, namchotsa iye: ndipo iye anamuka, nasocherera m'chipululu cha Beereseba.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ndipo Abrahamu analawira m'mamawa, natenga mkate ndi mchenje wa madzi, nampatsa Hagara, naika paphewa pake, ndi mwana, namchotsa iye: ndipo iye anamuka, nasocherera m'chipululu cha Beereseba.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 M'maŵa mwake, m'mamaŵa, Abrahamu adapatsa Hagara chakudya ndi thumba lachikopa la madzi. Kenaka adatenga mwanayo nabereketsa Hagara, ndipo atatero adamuuza kuti azipita. Hagara adachokadi, nkumangoyendayenda m'chipululu cha Beereseba.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Mmamawa wake, Abrahamu anatenga chakudya ndi botolo la madzi nazipereka kwa Hagara. Anasenzetsa Hagara nawaperekeza pangʼono ndi mnyamatayo. Hagara ananyamuka nayendayenda mʼchipululu cha Beeriseba.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 21:14
28 Mawu Ofanana  

Ndipo mthenga wa Yehova anampeza iye pa kasupe wa madzi m'chipululu, pa kasupe wa panjira ya ku Suri.


Ndipo Abrahamu analawira m'mamawa kunka kumalo kumene anaima pamaso pa Yehova:


Ndipo mwana wamwamuna wa mdzakazi uyo ndidzayesa mtundu, chifukwa iye ndiye mbeu yako.


Ndipo anatha madzi a m'thumba ndipo anaika mwana pansi pa chitsamba.


Chifukwa chake anatcha malowo Beereseba: chifukwa pamenepo analumbira onse awiri.


Ndipo Abrahamu anaoka mtengo wa bwemba pa Beereseba, naitanira pamenepo dzina la Yehova, Mulungu wa nthawi zonse.


Ndipo Abrahamu anabwera kwa anyamata ake, ndipo anauka nayenda pamodzi kumuka ku Beereseba; ndipo anakhala Abrahamu pa Beereseba.


Ndipo Abrahamu analawira m'mamawa namanga bulu wake, natengako anyamata ake awiri pamodzi naye, ndi Isaki mwana wake, nawaza nkhuni za nsembe yopsereza, nauka, nanka kumalo komwe Mulungu anamuuza iye.


Ndipo anadya namwa iye ndi anthu amene anali pamodzi naye, nagonapo usiku: ndipo anauka m'mamawa, ndipo iye anati, Mundilole ine ndinke kwa mbuyanga.


Koma kwa ana a akazi ake aang'ono amene Abrahamu anali nao Abrahamu anapatsa mphatso, nawachotsa iwo kwa Isaki mwana wake, akali ndi moyo, kuti anke kum'mawa, ku dziko la kum'mawa.


Ndipo analawira m'mamawa nalumbirirana wina ndi mnzake; ndipo Isaki anawalola amuke, ndipo anauka kuchokera kwa iye m'mtendere.


Ndipo anatcha dzina lake Siba, chifukwa chake dzina la mzindawo ndi Beereseba kufikira lero lino.


Yakobo ndipo anauka m'mamawa, natenga mwala umene anaika pansi pamutu wake, nauimiritsa, nathira mafuta pamutu pake.


Ndipo anampeza munthu, taonani, analinkusokera m'thengo; munthuyo ndipo anamfunsa, nati, Kodi ufuna chiyani?


Ndipo Israele anamuka ulendo wake ndi zonse anali nazo, nafika ku Beereseba, napereka nsembe kwa Mulungu wa Isaki atate wake.


Ndipo iye ataona chimenechi, ananyamuka, nathawa kupulumutsa moyo, nafika ku Beereseba wa ku Yuda, nasiya mnyamata wake pamenepo.


Pamenepo mfumu Hezekiya analawira mamawa, nasonkhanitsa akalonga a m'mzinda, nakwera kunka kunyumba ya Yehova.


Anasokera m'chipululu, m'njira yopanda anthu; osapeza mzinda wokhalamo.


Ndinafulumira, osachedwa, kusamalira malamulo anu.


Yemwe adalitsa mnzake ndi mau aakulu pouka mamawa, anthu adzachiyesa chimenecho temberero.


Monga mbalame yosochera kuchisa chake, momwemo munthu wosochera kumalo ake.


Chilichonse dzanja lako lichipeza kuchichita, uchichite ndi mphamvu yako; pakuti mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziwa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.


Pakuti minda ya ku Hesiboni yalefuka, ndi mpesa wa ku Sibima; ambuye a mitundu athyolathyola mitengo yosankhika yake; iwo anafikira ngakhale ku Yazere, nayendayenda m'chipululu; nthambi zake zinatasa, zinapitirira panyanja.


Koma kapolo sakhala m'nyumba nthawi yonse; mwana ndiye akhala nthawi yonse.


Ndipo Yoswa analawirira mamawa, kuchoka ku Sitimu, nafika ku Yordani, iye ndi ana onse a Israele; nagona komweko, asanaoloke.


Ndipo Samuele analawirira m'mawa kuti akakomane ndi Saulo; ndipo munthu anamuuza Samuele kuti, Saulo anafika ku Karimele, ndipo taonani, anaimika chikumbutso chake, nazungulira, napitirira, natsikira ku Giligala.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa