Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 21:15 - Buku Lopatulika

15 Ndipo anatha madzi a m'thumba ndipo anaika mwana pansi pa chitsamba.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Ndipo anatha madzi a m'mchenje ndipo anaika mwana pansi pa chitsamba.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Tsono madzi aja atamthera, adangosiya mwanayo pa chitsamba.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Madzi atatha mʼbotolo muja, anamuyika mnyamatayo pansi pa zitsamba.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 21:15
9 Mawu Ofanana  

Ndipo Abrahamu analawira m'mamawa, natenga mkate ndi thumba la madzi, nampatsa Hagara, naika paphewa pake, ndi mwana, namchotsa iye: ndipo iye anamuka, nasocherera m'chipululu cha Beereseba.


Ndipo ananka nakhala pansi popenyana naye patali, monga pakugwa muvi: chifukwa anati, Ndisaone kufa kwa mwana. Ndipo anakhala popenyana naye, nakweza mau ake nalira.


Nati iye, Pali Yehova Mulungu wako, ndilibe mkate, koma kaufa dzanja limodzi kali m'mbiya, ndi mafuta pang'ono m'nsupa; ndipo taona, ndilikutola nkhuni ziwiri kuti ndikadziphikire ndekha ndi mwana wanga, tidye, tife.


Namuka mfumu ya Israele, ndi mfumu ya Yuda, ndi mfumu ya Edomu, nazungulira njira ya masiku asanu ndi awiri; ndipo panalibe madzi kuti ankhondo amwe, kapena nyama zakuwatsata.


Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga; ndidzakufunani m'matanda kucha. Moyo wanga ukumva ludzu la kwa Inu, thupi langa lilirira Inu, m'dziko louma ndi lotopetsa, lopanda madzi.


Wachipala achita zake ndi nsompho, nagwira ntchito ndi makala, nafanizira fanolo ndi nyundo, nagwira ntchito yake ndi mkono wake wamphamvu; inde, ali ndi njala, ndipo mphamvu zake zilephera; iye samwa madzi, nalefuka.


Akulu ao atuma ang'ono ao kumadzi; afika kumaenje, osapeza madzi; abwera ndi mitsuko yao yopanda kanthu; ali ndi manyazi, athedwa nzeru, afunda mitu yao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa