Ndipo iye anati kwa iwo, Musandichedwetse ine, pakuti Yehova wandiyendetsa bwino m'njira yanga: mundilole ine ndinke kwa mbuyanga.
Genesis 24:54 - Buku Lopatulika Ndipo anadya namwa iye ndi anthu amene anali pamodzi naye, nagonapo usiku: ndipo anauka m'mamawa, ndipo iye anati, Mundilole ine ndinke kwa mbuyanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anadya namwa iye ndi anthu amene anali pamodzi naye, nagonapo usiku: ndipo anauka m'mamawa, ndipo iye anati, Mundilole ine ndinke kwa mbuyanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Wantchitoyo pamodzi ndi anthu amene anali nayewo adadya ndi kumwa, ndipo adagona komweko. Atadzuka m'maŵa, mlendoyo adati, “Loleni ndizibwerera kwa mbuyanga.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono wantchito uja ndi anthu amene anali naye anadya, kumwa nagona komweko. Kutacha mmawa wake, wantchito uja anati, “Mundilole ndibwerere kwa mbuye wanga.” |
Ndipo iye anati kwa iwo, Musandichedwetse ine, pakuti Yehova wandiyendetsa bwino m'njira yanga: mundilole ine ndinke kwa mbuyanga.
Ndipo anamlola Rebeka mlongo wao ndi mlezi wake, amuke pamodzi ndi mnyamata wake wa Abrahamu, ndi anthu ake.
Ndipo panali pamene Rakele anabala Yosefe, Yakobo anati kwa Labani, Undisudzule ine ndinke kwathu ku dziko langa.
Pomwepo Ahimaazi mwana wa Zadoki anati, Ndithamange nditengere mfumu mau kuti Yehova wabwezera chilango adani ake.
Kodi upenya munthu wofulumiza ntchito zake? Adzaima pamaso pa mafumu, osaima pamaso pa anthu achabe.
Usanene, Kodi bwanji masiku akale anapambana ano? Pakuti sulikufunsa mwanzeru pamenepo.