Genesis 24:5 - Buku Lopatulika Ndipo anati kwa iye mnyamatayo, Kapena sadzafuna mkaziyo kunditsata ine ku dziko lino: kodi ndikambwezerenso mwana wanu ku dziko komwe mwachokera inu? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anati kwa iye mnyamatayo, Kapena sadzafuna mkaziyo kunditsata ine ku dziko lino: kodi ndikambwezerenso mwana wanu ku dziko komwe mwachokera inu? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma wantchitoyo adafunsa kuti, “Nanga zidzatani mkaziyo akadzakana kubwera nane kuno? Kodi mwana wanuyo ndidzamperekeze ku dziko lanu kumene mudachokera?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Wantchito uja anafunsa kuti, “Nanga atakhala kuti mkaziyo sakufuna kubwera nane kuno? Kodi ine ndingadzatenge mwana wanu ndi kubwerera naye ku dziko kumene munachokera?” |
Ndipo anamuitana Rebeka nati kwa iye, Kodi udzanka pamodzi ndi munthuyo? Ndipo anati, Ndidzanka.
Usatchule dzina la Yehova Mulungu wako pachabe; chifukwa Yehova sadzamuyesa iye wosachimwa, amene atchula pachabe dzina lakelo.
Ndipo udzalumbira, Pali Yehova m'zoonadi, m'chiweruziro, ndi m'chilungamo; ndipo mitundu ya anthu idzadzidalitsa mwa Iye, ndipo mwa Iye adzatamandira.