Ndipo Yehova anavumbitsa pa Sodomu ndi pa Gomora miyala ya sulufure ndi moto kutuluka kwa Mulungu kumwamba;
Genesis 20:4 - Buku Lopatulika Koma Abimeleki sanayandikire naye; ndipo anati, Ambuye, kodi mudzaphanso mtundu wolungama? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Abimeleki sanayandikire naye; ndipo anati, Ambuye, kodi mudzaphanso mtundu wolungama? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Abimeleki anali asanamkhudze mkaziyo, choncho adati, “Ambuye, kodi Inu mungaphedi munthu wosalakwa? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nthawi imeneyi nʼkuti Abimeleki asanamukhudze mkaziyo, kotero kuti anati, “Ambuye, kodi mudzawonongadi mtundu wolungama? |
Ndipo Yehova anavumbitsa pa Sodomu ndi pa Gomora miyala ya sulufure ndi moto kutuluka kwa Mulungu kumwamba;
Kodi iye sanati kwa ine, Ndiye mlongo wanga: ndipo mkazi iye yekha anati, Iye ndiye mlongo wanga: ndi mtima wanga wangwiro ndi manja anga osachimwa ndachita ine ichi.
Ndipo Mulungu anati kwa iye m'kulota, Inde ndidziwa Ine, kuti wachita icho ndi mtima wangwiro, ndipo Inenso ndinakuletsa iwe kuti usandichimwire ine: chifukwa chake sindinakuloleze iwe kuti umkhudze mkaziyo.
Koposa kotani nanga, pamene anthu oipa anapha munthu wolungama pa kama wake m'nyumba yakeyake, ndidzafunsira mwazi wake ku dzanja lanu tsopano, ndi kukuchotsani ku dziko lapansi?
Ndipo Davide anati kwa Mulungu, Si ndine nanga ndalamulira kuti awerenge anthu? Inde, ndine amene ndachimwa ndi kuchita choipa ndithu; koma nkhosa izi zinachitanji? Dzanja lanu, Yehova Mulungu wanga, linditsutse ine ndi nyumba ya atate wanga, koma lisatsutse anthu anu ndi kuwachitira mliri.