Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 4:11 - Buku Lopatulika

11 Koposa kotani nanga, pamene anthu oipa anapha munthu wolungama pa kama wake m'nyumba yakeyake, ndidzafunsira mwazi wake ku dzanja lanu tsopano, ndi kukuchotsani ku dziko lapansi?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Koposa kotani nanga, pamene anthu oipa anapha munthu wolungama pa kama wake m'nyumba yakeyake, ndidzafunsira mwazi wake ku dzanja lanu tsopano, ndi kukuchotsani ku dziko lapansi?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Nanga nanji anthu oipa amene adapha munthu wopanda chifukwa ali gone m'nyumba mwake, kodi ndingapande kukulangani chifukwa cha imfa ya munthuyo, mpaka kukuchotsani pa dziko lapansi?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Nanji pamene anthu oyipa apha munthu wosalakwa ali mʼnyumba mwake ndiponso pa bedi lake! Kodi ine ndingaleke kukulangani ndi kukuchotsani pa dziko lapansi pano?”

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 4:11
19 Mawu Ofanana  

Tsopano ndiwe wotembereredwa kunthaka, imene inatsegula pakamwa pake kulandira padzanja lako mwazi wa mphwako:


Ndipo Mulungu anati kwa Nowa, Chimaliziro chake cha anthu onse chafika pamaso panga; pakuti dziko lapansi ladzala ndi chiwawa chifukwa cha iwo; taonani, ndidzaononga iwo pamodzi ndi dziko lapansi.


Ndipo zinaonongedwa zamoyo zonse zimene zinali padziko lapansi, anthu, ndi nyama, ndi zokwawa, ndi mbalame za m'mlengalenga; ndipo zinaonongedwa padziko lapansi: anatsala Nowa yekha ndi amene anali pamodzi naye m'chingalawa.


Yehova wabwezera pa iwe mwazi wonse wa nyumba ya Saulo, amene iwe wakhala mfumu m'malo mwake; ndipo Yehova wapereka ufumuwo m'dzanja la Abisalomu mwana wako; ndipo ona, wagwidwa m'kuipa kwako kwa iwe wekha, chifukwa uli munthu wa mwazi.


Pofikanso Abinere ku Hebroni, Yowabu anampambutsa kupita naye pakati pa chipata kulankhula naye poduka mphepo; namgwaza pomwepo m'mimba, nafa, chifukwa cha mwazi wa Asahele mbale wake.


Ndipo ndikali wofooka ine lero, chinkana ndinadzozedwa mfumu; ndipo ana aamuna awa a Zeruya andikakalira mtima; Yehova abwezere wochita choipa monga mwa choipa chake.


Ndipo Yehova adzambwezera mwazi wake pamutu wake wa iye yekha, popeza iye anawakantha anthu awiri olungama ndi okoma oposa iye mwini, nawapha ndi lupanga, atate wanga Davide osadziwa, ndiwo Abinere mwana wa Nere kazembe wa khamu la nkhondo la Israele, ndi Amasa mwana wa Yetere kazembe wa khamu la nkhondo la Yuda.


Zikhale pamaso pa Yehova chikhalire, kuti adule chikumbukiro chao kuchichotsera kudziko lapansi.


Pakuti Iye wofuna chamwazi awakumbukira; saiwala kulira kwa ozunzika.


Iye amene akantha munthu kotero kuti wafa, aphedwe ndithu.


Pakuti ndatambasula dzanja langa tsopano, kuti ndikupande iwe ndi anthu ako ndi mliri, ndi kuti uonongeke padziko lapansi.


Koma oipa adzalikhidwa m'dziko, achiwembu adzazulidwamo.


Monga kasupe wopondedwa, ndi chitsime choonongeka, momwemo wolungama ngati agonjera woipa.


Muzitero nao, milungu imene sinalenge miyamba ndi dziko lapansi, iyo idzatha kudziko lapansi, ndi pansi pa miyambayo.


Si ndinu wachikhalire, Yehova Mulungu wanga, wopatulika wanga? Sitidzafa. Yehova munamuikiratu kuti aweruzidwe; ndipo Inu, Thanthwe, munamkhazika kuti alangidwe.


Pakuti chilamulo chalekeka, ndi chiweruzo sichitulukira konse; popeza woipa azinga wolungama, chifukwa chake chiweruzo chituluka chopindika.


osati monga Kaini anali wochokera mwa woipayo, namupha mbale wake. Ndipo anamupha Iye chifukwa ninji? Popeza ntchito zake zinali zoipa, ndi za mbale wake zolungama.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa