Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 4:12 - Buku Lopatulika

12 Ndipo Davide analamulira anyamata ake, iwo nawapha, nawapachika m'mbali mwa thamanda ku Hebroni atawadula manja ndi mapazi ao. Koma mutu wa Isiboseti anautenga nauika m'manda a Abinere ku Hebroni.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo Davide analamulira anyamata ake, iwo nawapha, nawapachika m'mbali mwa thamanda ku Hebroni atawadula manja ndi mapazi ao. Koma mutu wa Isiboseti anautenga nauika m'manda a Abinere ku Hebroni.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Motero Davide adalamula ankhondo ake, ndipo adaŵapha anthuwo, naŵadula manja ndi mapazi, naŵapachika pambali pa dziŵe la ku Hebroni. Koma adatenga mutu wa Isiboseti, nakauika m'manda a Abinere ku Hebroni.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Kotero Davide analamulira ankhondo ake, ndipo anawapha. Iwo anawadula manja ndi mapazi ndi kupachika matupi awo pa dziwe la ku Hebroni. Koma anatenga mutu wa Isi-Boseti nawuyika mʼmanda a Abineri ku Hebroni.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 4:12
8 Mawu Ofanana  

Davide naitana wina wa anyamatawo, nati, Sendera numkanthe. Ndipo anamkantha, nafa iye.


Yehova wabwezera pa iwe mwazi wonse wa nyumba ya Saulo, amene iwe wakhala mfumu m'malo mwake; ndipo Yehova wapereka ufumuwo m'dzanja la Abisalomu mwana wako; ndipo ona, wagwidwa m'kuipa kwako kwa iwe wekha, chifukwa uli munthu wa mwazi.


Koma Abinere, mwana wa Nere, kazembe wa khamu la ankhondo a Saulo anatenga Isiboseti mwana wa Saulo, namuolotsa nanka naye ku Mahanaimu;


niwapereka m'manja a Agibiyoni, iwo nawapachika m'phiri pamaso pa Yehova, ndipo anagwa pamodzi onse asanu ndi awiri; m'masiku a kukolola, m'masiku oyamba, poyamba kucheka barele.


Ndipo anaika Abinere ku Hebroni; ndi mfumu inakweza mau ake nilira ku manda a Abinere, nalira anthu onse.


Koma Inu, Mulungu, mudzawatsitsira kudzenje la chionongeko. Anthu okhetsa mwazi ndi achinyengo masiku ao sadzafikira nusu; koma ine ndidzakhulupirira Inu.


Pakuti ndi kuweruza kumene muweruza nako, inunso mudzaweruzidwa; ndipo ndi muyeso umene muyesa nao, kudzayesedwa kwa inunso.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa