Ndipo linalinkulowa dzuwa, ndi tulo tatikulu tinamgwera Abramu: ndipo taonani, kuopsa kwa mdima waukulu kunamgwera iye.
Genesis 2:21 - Buku Lopatulika Koma Yehova Mulungu anamgonetsa Adamu tulo tatikulu, ndipo anagona; ndipo anatengako nthiti yake imodzi, natsekapo ndi mnofu pamalo pake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Yehova Mulungu anamgonetsa Adamu tulo tatikulu, ndipo anagona; ndipo anatengako nthiti yake imodzi, natsekapo ndi mnofu pamalo pake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Chauta adagonetsa Adamu tulo tofanato, ndipo ali m'tulo choncho, Mulungu adamchotsako nthiti, natsekapo ndi mnofu pamalopo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono Yehova Mulungu anamugonetsa munthu uja tulo tofa nato; ali mtulo chomwecho, Mulungu anachotsa imodzi mwa nthiti zake ndi kutseka pamalopo ndi mnofu. |
Ndipo linalinkulowa dzuwa, ndi tulo tatikulu tinamgwera Abramu: ndipo taonani, kuopsa kwa mdima waukulu kunamgwera iye.
M'kulota, m'masomphenya a usiku, pakuwagwera anthu tulo tatikulu, pogona mwatcheru pakama,
Ndipo m'mene analikulankhula ndi ine ndinagwidwa ndi tulo tatikulu, nkhope yanga pansi; koma anandikhudza, nandiimiritsa pokhala inepo.
Chomwecho Davide anatenga mkondowo, ndi chikho cha madzi ku mutu wa Saulo nachoka iwowa, osawaona munthu, kapena kuzidziwa, kapena kugalamuka; pakuti onse anali m'tulo; popeza tulo tatikulu tochokera kwa Yehova tinawagwira onse.