Ndipo anati Mulungu, Taonani, ndakupatsani inu therere lonse lakubala mbeu lili padziko lapansi, ndi mitengo yonse m'mene muli chipatso cha mtengo wakubala mbeu; chidzakhala chakudya cha inu:
Genesis 2:16 - Buku Lopatulika Ndipo Yehova Mulungu anamuuza munthuyo, nati, Mitengo yonse ya m'munda udyeko; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova Mulungu anamuuza munthuyo, nati, Mitengo yonse ya m'munda udyeko; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo Chauta adamlamula munthuyo kuti, “Uzidya zipatso za mtengo uliwonse wam'mundawu, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Yehova Mulungu analamula munthu uja kuti, “Uzidya zipatso za mu mtengo wina uliwonse mʼmundamu; |
Ndipo anati Mulungu, Taonani, ndakupatsani inu therere lonse lakubala mbeu lili padziko lapansi, ndi mitengo yonse m'mene muli chipatso cha mtengo wakubala mbeu; chidzakhala chakudya cha inu:
Ndipo Yehova Mulungu anatenga munthuyo, namuika iye m'munda wa Edeni kuti aulime nauyang'anire.
Ndipo Yehova Mulungu anameretsa m'nthaka mitengo yonse yokoma m'maso ndi yabwino kudya; ndiponso mtengo wa moyo pakati pamundapo, ndi mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa.
Koma zipatso za mtengo umene uli m'kati mwa munda, Mulungu anati, Musadye umenewo, musakhudze umenewo, mungadzafe.
Pakuti cholengedwa chonse cha Mulungu nchabwino, ndipo palibe kanthu kayenera kutayika, ngati kalandiridwa ndi chiyamiko;
Lamulira iwo achuma m'nthawi ino ya pansi pano, kuti asadzikuze, kapena asayembekezere chuma chosadziwika kukhala kwake, koma Mulungu, amene atipatsa ife zonse kochulukira, kuti tikondwere nazo;
Ndipo Samuele anati, Kodi Yehova akondwera ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zophera, monga ndi kumvera mau a Yehova? Taonani, kumvera ndiko kokoma koposa nsembe, kutchera khutu koposa mafuta a nkhosa zamphongo.