Ndipo Abrahamu adagwa nkhope pansi, naseka, nati m'mtima mwake, Kodi mwana adzabadwa kwa iye amene ali wa zaka zana? Kodi Sara wa zaka makumi asanu ndi anai adzabala?
Genesis 17:18 - Buku Lopatulika Ndipo Abrahamu anati kwa Mulungu, Ha! Ismaele akhale ndi moyo pamaso panu! Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Abrahamu anati kwa Mulungu, Ha! Ismaele akhale ndi moyo pamaso panu! Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo adauza Mulungu kuti, “Ndikukupemphani kuti mungodalitsa Ismaele yemweyu.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Abrahamu anati kwa Mulungu, “Bwanji mumudalitse Ismaeli.” |
Ndipo Abrahamu adagwa nkhope pansi, naseka, nati m'mtima mwake, Kodi mwana adzabadwa kwa iye amene ali wa zaka zana? Kodi Sara wa zaka makumi asanu ndi anai adzabala?
Ndipo Mulungu anati, Koma Sara mkazi wako adzakubalira iwe mwana wamwamuna; ndipo udzamutcha dzina lake Isaki; ndipo ndidzalimbikitsa naye pangano langa, kuti likhale pangano la nthawi zonse, la ku mbeu zake za pambuyo pake.
pamene udzalima panthaka siidzaperekanso kwa iwe mphamvu yake: udzakhala wothawathawa ndi woyendayenda padziko lapansi.
Taonani, mwandiingitsa ine lero lomwe padziko; ndi pankhope panu ndidzabisika; ndipo ndidzakhala wothawathawa ndi woyendayenda padziko lapansi; ndipo kudzatero kuti onse akundipeza adzandipha.
Ambiri amati, Adzationetsa chabwino ndani? Weramutsirani ife kuunika kwa nkhope yanu, Yehova.
Ndipo ine, mundigwirizize mu ungwiro wanga, ndipo mundiike pankhope panu kunthawi yamuyaya.
koma zoipa zanu zakulekanitsani inu ndi Mulungu wanu; ndipo machimo anu abisa nkhope yake kwa inu, kuti Iye sakumva.
ndipo ndidzawapatsa mtima umodzi ndi njira imodzi, kuti andiope Ine masiku onse; kuwachitira zabwino, ndi ana ao pambuyo pao;
Pakuti lonjezano lili kwa inu, ndi kwa ana anu, ndi kwa onse akutali, onse amene Ambuye Mulungu wathu adzaitana.