Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 41:12 - Buku Lopatulika

12 Ndipo ine, mundigwirizize mu ungwiro wanga, ndipo mundiike pankhope panu kunthawi yamuyaya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo ine, mundigwirizize m'ungwiro wanga, ndipo mundiike pankhope panu kunthawi yamuyaya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Inu mwandichirikiza chifukwa cha kukhulupirika kwanga, mwandikhazika pamaso panu mpaka muyaya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Mu ungwiro wanga Inu mumandisunga ndi kundiyimika pamaso panu kwamuyaya.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 41:12
11 Mawu Ofanana  

Sawachotsera wolungama maso ake, koma pamodzi ndi mafumu pa mpando wao awakhazika chikhazikire, ndipo akwezeka.


Mudzandidziwitsa njira ya moyo, pankhope panu pali chimwemwe chokwanira; m'dzanja lanu lamanja muli zokondweretsa zomka muyaya.


Koma ine ndidzapenyerera nkhope yanu m'chilungamo, ndidzakhuta mtima ndi maonekedwe anu, pamene ndidzauka.


Ungwiro ndi kuongoka mtima zindisunge, pakuti ndayembekezera Inu.


Yehova, Mulungu wanga, ndinafuulira kwa Inu, ndipo munandichiritsa.


Maso a Yehova ali pa olungama mtima, ndipo makutu ake atchereza kulira kwao.


Pakuti manja a oipa adzathyoledwa, koma Yehova achirikiza olungama.


Moyo wanga uumirira Inu. Dzanja lamanja lanu lindigwiriziza.


Pamene ndinati, Literereka phazi langa, chifundo chanu, Yehova, chinandichirikiza.


Atate, amene mwandipatsa Ine, ndifuna kuti, kumene ndili Ine, iwonso akhale pamodzi ndi Ine; kuti ayang'anire ulemerero wanga, umene mwandipatsa Ine; pakuti munandikonda Ine lisanakhazikike dziko lapansi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa