Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Genesis 15:8 - Buku Lopatulika

Ndipo anati, Ambuye Mulungu, nanga ndidzadziwa bwanji kuti lidzakhala cholowa changa?

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo anati, Ambuye Mulungu, nanga ndidzadziwa bwanji kuti lidzakhala cholowa changa?

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Koma Abramu adati, “Ambuye Chauta, kodi ndingadziŵe bwanji kuti dziko limeneli lidzakhaladi langa?”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Koma Abramu anati, “Haa! Ambuye Yehova, kodi ndingadziwe bwanji kuti lidzakhaladi langa?”

Onani mutuwo



Genesis 15:8
15 Mawu Ofanana  

Ndipo anati kwa iye, Kanditengere Ine ng'ombe yaikazi ya zaka zitatu, ndi mbuzi yaikazi ya zaka zitatu, ndi tonde wa zaka zitatu, ndi njiwa, ndi bunda.


akupatse iwe mdalitso wa Abrahamu, iwe ndi mbeu zako pamodzi nawe: kuti ulowe m'dziko limene ukhalamo mlendo, limene Mulungu anampatsa Abrahamu.


Yosefe ndipo anati kwa abale ake, Ndilinkufa ine, koma Mulungu adzaonekera kwa inu, adzakuchotsani inu m'dziko muno kubwera kunka ku dziko limene analumbirira kwa Abrahamu ndi kwa Isaki, ndi kwa Yakobo.


Nati Hezekiya kwa Yesaya, Chizindikiro chake nchiyani kuti Yehova adzandichiza, ndi kuti ndidzakwera kunka kunyumba ya Yehova tsiku lachitatu?


Mundichitire chizindikiro choti chabwino; kuti ondida achione, nachite manyazi, popeza Inu, Yehova, munandithandiza ndi kundisangalatsa.


Udzipemphere wekha chizindikiro cha kwa Yehova Mulungu wako; pempha cham'mwakuya, kapena cham'mwamba.


Ndipo ndidzapereka anthu akulakwira pangano langa, amene sanachite mau a pangano limene anapangana pamaso panga, muja anadula pakati mwanawang'ombe ndi kupita pakati pa mbali zake;


akulu a Yuda, ndi akulu a Yerusalemu, adindo, ndi ansembe, ndi anthu onse a m'dziko, amene anapita pakati pa mbali za mwanawang'ombe;


Ndipo Zekariya anati kwa mngelo, Ndidzadziwitsa ichi ndi chiyani? Pakuti ndine nkhalamba, ndipo zaka zake za mkazi wanga zachuluka.


Koma Maria anati kwa mngelo, Ichi chidzachitika bwanji, popeza ine sindidziwa mwamuna?