Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 20:8 - Buku Lopatulika

8 Nati Hezekiya kwa Yesaya, Chizindikiro chake nchiyani kuti Yehova adzandichiza, ndi kuti ndidzakwera kunka kunyumba ya Yehova tsiku lachitatu?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Nati Hezekiya kwa Yesaya, Chizindikiro chake nchiyani kuti Yehova adzandichiza, ndi kuti ndidzakwera kunka kunyumba ya Yehova tsiku lachitatu?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Apo Hezekiya adafunsa Yesaya uja kuti, “Kodi padzakhala chizindikiro chanji choonetsa kuti Chauta adzandichiritsa, ndipo kuti ndidzatha kukapembedza ku Nyumba ya Chauta mkucha uno?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Tsono Hezekiya anafunsa Yesaya kuti, “Kodi padzakhala chizindikiro chanji choonetsa kuti Yehova adzandichiritsa ndi kuti ndidzapita ku Nyumba ya Yehova pa tsiku lachitatu kuchokera lero lino?”

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 20:8
14 Mawu Ofanana  

Ndipo anati, Ambuye Mulungu, nanga ndidzadziwa bwanji kuti lidzakhala cholowa changa?


Ndi ichi ndi chizindikiro chako: chaka chino mudzadya za mphulumukwa, ndi chaka cha mawa za mankhokwe, ndi chaka chamkucha muzibzala ndi kukolola, muzioka minda yampesa ndi kudya zipatso zake.


Bwerera, nunene kwa Hezekiya mtsogoleri wa anthu anga, Atero Yehova Mulungu wa Davide kholo lako, Ndamva pemphero lako, ndapenya misozi yako; taona, ndidzakuchiritsa, tsiku lachitatu udzakwera kunka kunyumba ya Yehova.


Nati Yesaya, Tenga nchinchi yankhuyu. Naitenga, naiika pafundo, nachira iye.


Nati Yesaya, Chizindikiro ndichi akupatsa Yehova, kuti Yehova adzachichita chonena Iye; kodi mthunzi umuke m'tsogolo makwerero khumi, kapena ubwerere m'mbuyo makwerero khumi?


Ndipo Yesaya adati, Atenge m'bulu wankhuyu, auike pafundo, ndipo iye adzachira.


Hezekiya anatinso, Chizindikiro nchiyani, kuti ndidzakwera kunka kunyumba ya Yehova?


Udzipemphere wekha chizindikiro cha kwa Yehova Mulungu wako; pempha cham'mwakuya, kapena cham'mwamba.


Chifukwa chake Ambuye mwini yekha adzakupatsani inu chizindikiro; taonani namwali adzaima, nadzabala mwana wamwamuna, nadzamutcha dzina lake Imanuele.


Atapita masiku awiri adzatitsitsimutsa, tsiku lachitatu adzatiutsa; ndipo tidzakhala ndi moyo pamaso pake.


Anthu awiri anakwera kunka ku Kachisi kukapemphera; winayo Mfarisi ndi mnzake wamsonkho.


Ndipo ichi ndi chizindikiro kwa inu: Mudzapeza mwana wakhanda wokuta ndi nsalu atagona modyera.


Ndipo anati kwa Iye, Ngati mundikomera mtima mundionetse chizindikiro tsopano chakuti ndi Inu wakunena nane.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa