Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 15:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo anati kwa iye, Ine ndine Yehova amene ndinatulutsa iwe mu Uri wa kwa Akaldeya, kuti ndikupatse iwe dziko limeneli likhale lakolako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo anati kwa iye, Ine ndine Yehova amene ndinatulutsa iwe m'Uri wa kwa Akaldeya, kuti ndikupatse iwe dziko limeneli likhale lakolako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Tsono Chauta adamuuza kuti, “Ine ndine Chauta amene ndidakutulutsa ku Uri wa ku Kaldeya, kuti ndikupatse dziko lino kuti likhale lakolako.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Ndipo anamuwuza kuti, “Ine ndine Yehova amene ndinakuchotsa iwe ku mzinda wa Uri wa ku Akaldeya kuti ndikupatse dziko ili kuti likhale lako.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 15:7
16 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova anati kwa Abramu, Tuluka iwe m'dziko lako, ndi kwa abale ako, ndi kunyumba ya atate wako, kunka ku dziko limene ndidzakusonyeza iwe;


Ndipo Yehova anaonekera kwa Abramu nati, Ndidzapatsa mbeu yako dziko lino: pamenepo anammangira Yehova guwa la nsembe amene anamuonekera iye.


akupatse iwe mdalitso wa Abrahamu, iwe ndi mbeu zako pamodzi nawe: kuti ulowe m'dziko limene ukhalamo mlendo, limene Mulungu anampatsa Abrahamu.


Yosefe ndipo anati kwa abale ake, Ndilinkufa ine, koma Mulungu adzaonekera kwa inu, adzakuchotsani inu m'dziko muno kubwera kunka ku dziko limene analumbirira kwa Abrahamu ndi kwa Isaki, ndi kwa Yakobo.


Ndi kunena kuti, Ndidzakupatsa iwe dziko la Kanani, gawo la cholowa chako;


Popeza anakumbukira mau ake oyera, ndi Abrahamu mtumiki wake.


Ndipo anawapatsa maiko a amitundu; iwo ndipo analanda zipatso za ntchito ya anthu:


Kumbukirani Abrahamu, Isaki ndi Israele, atumiki anu, amene munawalumbirira ndi kudzitchula nokha, amene munanena nao, Ndidzachulukitsa mbeu zanu ngati nyenyezi za kuthambo, ndi dziko ili lonse ndanenali ndidzapatsa mbeu zanu, likhale cholowa chao nthawi zonse.


ndipo mulande dziko, ndi kukhala m'mwemo, pakuti ndinakupatsani inu dzikoli likhale lanulanu.


Pakuti lonjezo lakuti iye adzakhala wolowa nyumba wa dziko lapansi silinapatsidwe kwa Abrahamu ndi kwa mbeu yake mwa lamulo, koma mwa chilungamo cha chikhulupiriro.


Ndipo ndinauza inu muja, ndi kuti, Yehova Mulungu wanu wakupatsani dziko ili likhale lanulanu, muoloke, amuna onse amphamvu ovala zida zao, pamaso pa abale anu ana a Israele.


Simulowa kulandira dziko lao chifukwa cha chilungamo chanu, kapena mtima wanu woongoka; koma Yehova Mulungu wanu awapirikitsa pamaso panu chifukwa cha zoipa za amitundu awa, ndi kuti akhazikitse mau amene Yehova analumbirira makolo anu, Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa