Ndipo malire a Akanani anayamba pa Sidoni, pakunka ku Gerari ndi ku Gaza; pakunka ku Sodomu, ndi ku Gomora, ndi Adima, ndi Zeboimu, kufikira ku Lasa.
Genesis 14:2 - Buku Lopatulika iwo anathira nkhondo pa Bera mfumu ya Sodomu, ndi pa Birisa, mfumu ya Gomora, ndi pa Sinabe mfumu ya Adima, ndi pa Semebera mfumu ya Zeboimu, ndi pa mfumu ya Bela (kumeneko ndi ku Zowari). Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 iwo anathira nkhondo pa Bera mfumu ya Sodomu, ndi pa Birisa, mfumu ya Gomora, ndi pa Sinabe mfumu ya Adima, ndi pa Semebera mfumu ya Zeboimu, ndi pa mfumu ya Bela (kumeneko ndi ku Zowari). Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa onseŵa adasonkhana kuti athire nkhondo mafumu asanu aŵa: Mfumu Bera wa ku Sodomu, mfumu Birisa wa ku Gomora, mfumu Sinabe wa ku Adima, mfumu Semebera wa ku Zeboimu ndi mfumu ya ku Bela (ndiye kuti Zowari). Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero anathira nkhondo Bera mfumu ya ku Sodomu, Birisa mfumu ya Gomora, Sinabi mfumu ya Adima, Semeberi mfumu ya Ziboimu ndi mfumu ya Bela (kumeneko ndi ku Zowari). |
Ndipo malire a Akanani anayamba pa Sidoni, pakunka ku Gerari ndi ku Gaza; pakunka ku Sodomu, ndi ku Gomora, ndi Adima, ndi Zeboimu, kufikira ku Lasa.
Ndipo Loti anatukula maso ake nayang'ana chigwa chonse cha Yordani kuti chonsecho chinali ndi madzi ambiri, asanaononge Yehova Sodomu ndi Gomora, monga munda wa Yehova, monga dziko la Ejipito pakunka ku Zowari.
Ndipo Abramu anakhala m'dziko la Kanani, ndipo Loti anakhala m'mizinda ya m'chigwa, nasendeza hema wake kufikira ku Sodomu.
Mtima wanga ufuula chifukwa cha Mowabu: akulu ake athawira ku Zowari, ku Egilati-Selisiya; pakuti pa chikweza cha Luhiti akwera alikulira, pakuti m'njira ya Horonaimu akweza mfuu wa chionongeko.
Kuyambira kufuula kwa Hesiboni mpaka ku Eleyale, mpaka ku Yahazi anakweza mau, kuyambira pa Zowari mpaka ku Horonaimu, ku Egilati-Selisiya; pakuti pamadzi a ku Nimurimu komwe padzakhala mabwinja.
Ndidzakusiya bwanji, Efuremu? Ndidzakupereka bwanji, Israele? Ndidzakuyesa bwanji ngati Adima? Ndidzakuika bwanji ngati Zeboimu? Mtima wanga watembenuka m'kati mwanga, zachifundo zanga zilira zonse pamodzi.
Ndi kuti lidapsa dziko lake lonse ndi sulufure, ndi mchere, kuti sabzalamo, kapena siliphukitsa kanthu kapena sumerapo msipu, monga kupasula kwake kwa Sodomu ndi Gomora, Adima, ndi Zeboimu, imene Yehova anaipasula m'mkwiyo wake ndi ukali wake;
ndi kumwera, ndi chidikha cha chigwa cha Yeriko, mzinda wa migwalangwa, kufikira ku Zowari.
gulu lina linalowa njira yonka ku Betehoroni; ndi gulu linanso linalowa ku njira ya kumalire, akuyang'ana ku chigwa cha Zeboimu kuchipululuko.