Genesis 10:7 - Buku Lopatulika Ndi ana aamuna a Kusi: Seba, ndi Havila, ndi Sabita, ndi Raama, ndi Sabiteka; ndi ana a Raama: Sheba ndi Dedani. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndi ana amuna a Kusi: Seba, ndi Havila, ndi Sabita, ndi Raama, ndi Sabiteka; ndi ana a Raama: Sheba ndi Dedani. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ana a Kusi anali Seba, Havila, Sabita, Raama ndi Sabiteka. Ana a Raama anali Sheba ndi Dedani. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ana aamuna a Kusi anali: Seba, Havila, Sabita, Raama ndi Sabiteka. Ana aamuna a Raama anali: Seba ndi Dedani. |
Dzina la woyamba ndi Pisoni: umenewo ndiwo wozungulira dziko lonse la Havila, m'mene muli golide;
Ndipo atamva mfumu yaikazi ya ku Sheba mbiri ya Solomoni yakubukitsa dzina la Yehova, anadza kumuyesera iye ndi miyambi yododometsa.
Ndi ana a Kusi: Seba, ndi Havila, ndi Sabita, ndi Raama, ndi Sabiteka. Ndi ana a Raama: Sheba, ndi Dedani.
koma anazigwera Aseba, nazitenga, nawapha anyamata ndi lupanga lakuthwa, ndipo ndapulumuka ine ndekha kudzakuuzani.
Mafumu a ku Tarisisi ndi ku Zisumbuzo adzabwera nacho chopereka; mafumu a ku Sheba ndi Seba adzadza nazo mphatso.
Katundu wa pa Arabiya. M'nkhalango ya mu Arabiya mudzagona, inu makamu oyendayenda a Dedani.
Chifukwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wako, Woyera wa Israele, Mpulumutsi wako; ndapatsa Ejipito dombolo lako, Etiopiya ndi Seba m'malo mwako.
Anthu a ku Dedani anakutsatsa malonda, zisumbu zambiri zinazolowerana nawe malonda ako, anabwera nazo minyanga ndi phingo kugulana nawe malonda.
Amalonda a ku Sheba ndi a ku Raama anagulana nawe malonda; anagula malonda ako ndi zonunkhira zoposa zilizonse, ndi miyala iliyonse ya mtengo wake, ndi golide.