Pakuti ndingakhale ndikadzitamandira kanthu kochulukira za ulamuliro (umene anatipatsa Ambuye kukumangirira, ndipo si kukugwetsera kwanu), sindidzanyazitsidwa;
Filemoni 1:8 - Buku Lopatulika Momwemo, ndingakhale ndili nako kulimbika mtima kwakukulu mu Khristu kukulamulira chimene chiyenera, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Momwemo, ndingakhale ndili nako kulimbika mtima kwakukulu m'Khristu kukulamulira chimene chiyenera, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono, inde nkotheka kuti ndichite kukulamula m'dzina la Khristu zimene uyenera kuchita. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsopano ngakhale kuti mwa Khristu nditha kulimba mtima ndi kulamulira kuti uchite zimene uyenera kuchita, |
Pakuti ndingakhale ndikadzitamandira kanthu kochulukira za ulamuliro (umene anatipatsa Ambuye kukumangirira, ndipo si kukugwetsera kwanu), sindidzanyazitsidwa;
Ndinena monga mwa kunyoza, monga ngati tinakhala ofooka. Koma m'mene wina alimbika mtimamo (ndinena mopanda nzeru) momwemo ndilimbika mtima inenso.
kapena chinyanso, ndi kulankhula zopanda pake, kapena zopusa zimene siziyenera; koma makamaka chiyamiko.
koma tingakhale tidamva zowawa kale, ndipo anatichitira chipongwe, monga mudziwa, ku Filipi, tinalimbika pakamwa mwa Mulungu wathu kulankhula ndi inu Uthenga Wabwino wa Mulungu m'kutsutsana kwambiri.
kapena sitinakhale ofuna ulemerero wa kwa anthu, kapena kwa inu, kapena kwa ena, tingakhale tinali nayo mphamvu yakukulemetsani monga atumwi a Khristu.