Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Filemoni 1:8 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Tsopano ngakhale kuti mwa Khristu nditha kulimba mtima ndi kulamulira kuti uchite zimene uyenera kuchita,

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

8 Momwemo, ndingakhale ndili nako kulimbika mtima kwakukulu mu Khristu kukulamulira chimene chiyenera,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Momwemo, ndingakhale ndili nako kulimbika mtima kwakukulu m'Khristu kukulamulira chimene chiyenera,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Tsono, inde nkotheka kuti ndichite kukulamula m'dzina la Khristu zimene uyenera kuchita.

Onani mutuwo Koperani




Filemoni 1:8
7 Mawu Ofanana  

Tsono ngakhale nditadzitama momasuka za ulamuliro umene Ambuye anatipatsa woti tikukuzeni osati kukuwonongani, ndithu sindidzachita manyazi.


Ndikuvomera mwamanyazi kuti ife sitinali olimba mtima kuti nʼkuchita zinthu zimenezi. Ndikuyankhula ngati chitsiru kuti chimene wina aliyense akhoza kudzitama nacho, Inenso ndikhoza kudzitama nachonso.


Choncho, popeza tili ndi chiyembekezo chotere, ndife olimba mtima kwambiri.


Musamatukwane, kuyankhula zopusa kapena kunena nthabwala zopanda pake, zomwe ndi zosayenera, koma mʼmalo mwake muziyamika.


Monga mukudziwa, ife nʼkuti titazunzika ndi kunyozedwa ku Filipi. Koma mothandizidwa ndi Mulungu wathu, tinalimba mtima mpaka kukulalikirani uthenga wake wabwino ngakhale ambiri ankatsutsana nafe.


Ife sitinafune kutamidwa ndi anthu, kapena ndi inu, kapena wina aliyense mwa inu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa