Wamphamvuyonse alekeranji kuikiratu nyengo? Ndi iwo omdziwa alekeranji kudziwa masiku ake?
Eksodo 9:5 - Buku Lopatulika Ndipo Yehova anaika nthawi yakuti, nati, Mawa Yehova adzachita chinthu ichi m'dzikomu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova anaika nthawi yakuti, nati, Mawa Yehova adzachita chinthu ichi m'dzikomu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta waika nthaŵi, ndipo akunena kuti zimenezi azichita maŵa.’ ” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova anayika nthawi ndipo anati, “Yehova adzachita zimenezi mmawa mʼdziko muno.” |
Wamphamvuyonse alekeranji kuikiratu nyengo? Ndi iwo omdziwa alekeranji kudziwa masiku ake?
Ndipo ndidzaika chosiyanitsa pakati pa anthu anga ndi anthu ako; mawa padzakhala chizindikiro ichi.
Taona, mawa monga nthawi ino ndidzavumbitsa mvumbi wa matalala, sipadakhale unzake mu Ejipito kuyambira tsiku lija lidakhazikika kufikira lero lino.
Ndipo Yehova adzasiyanitsa pakati pa zoweta za Israele ndi zoweta za Ejipito; kuti kasafe kanthu kalikonse ka ana a Israele.
Ndipo m'mawa mwake Yehova anachita chinthucho, ndipo zinafa zoweta zonse za mu Ejipito; koma sichinafe chimodzi chonse cha zoweta za ana a Israele.
nanena ndi Kora ndi khamu lake lonse, ndi kuti, M'mawa Yehova adzatizindikiritsa anthu ake ndi ayani, wopatulika ndani, amene adzamsendeza pafupi pa Iye; ndi iye amene anamsankha adzamsendeza pafupi pa Iye.