niwapereka m'manja a Agibiyoni, iwo nawapachika m'phiri pamaso pa Yehova, ndipo anagwa pamodzi onse asanu ndi awiri; m'masiku a kukolola, m'masiku oyamba, poyamba kucheka barele.
Eksodo 9:31 - Buku Lopatulika Ndipo thonje ndi barele zinayoyoka; pakuti barele lidafula, ndi thonje lidayamba maluwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo thonje ndi barele zinayoyoka; pakuti barele lidafula, ndi thonje lidayamba maluwa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo thonje lidaonongeka pamodzi ndi barele yemwe, chifukwa choti bareleyo anali atacha, ndipo thonjelo linali ndi nkhunje. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Thonje ndi barele zinawonongeka, popeza barele anali atakhwima ndi thonje linali ndi maluwa. |
niwapereka m'manja a Agibiyoni, iwo nawapachika m'phiri pamaso pa Yehova, ndipo anagwa pamodzi onse asanu ndi awiri; m'masiku a kukolola, m'masiku oyamba, poyamba kucheka barele.
Ndinakukanthani ndi chinsikwi ndi chinoni; minda yanu yochuluka yamipesa, ndi yamikuyu, ndi ya azitona, yaonongeka ndi dzombe; koma simunabwerere kudza kwa Ine, ati Yehova.
Chinkana mkuyu suphuka, kungakhale kulibe zipatso kumpesa; yalephera ntchito ya azitona, ndi m'minda m'mosapatsa chakudya; ndi zoweta zachotsedwa kukhola, palibenso ng'ombe m'makola mwao;
Momwemo anabwera Naomi ndi Rute Mmowabu mpongozi wake pamodzi naye, amene anabwera kuchokera ku dziko la Mowabu; ndipo anafika ku Betelehemu, pakuyamba anthu kucheka barele.
Momwemo anaumirira adzakazi a Bowazi kuti atole khunkha kufikira atatha kucheka barele ndi tirigu; ndipo anakhala iye kwao kwa mpongozi wake.