Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Rute 2:23 - Buku Lopatulika

23 Momwemo anaumirira adzakazi a Bowazi kuti atole khunkha kufikira atatha kucheka barele ndi tirigu; ndipo anakhala iye kwao kwa mpongozi wake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Momwemo anaumirira adzakazi a Bowazi kuti atole khunkha kufikira atatha kucheka barele ndi tirigu; ndipo anakhala iye kwao kwa mpongozi wake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Motero Rute ankatsatira adzakazi a Bowaziwo, namakunkha, mpaka anthu atamaliza kudula barele ndi tirigu. Monsemo Rute ankakhala ndi mpongozi wakeyo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Choncho Rute ankatsatira adzakazi a Bowazi namakunkha mpaka anthu atamaliza kudula barele ndi tirigu. Ndipo amakhalabe ndi mpongozi wakeyo.

Onani mutuwo Koperani




Rute 2:23
11 Mawu Ofanana  

Ndipo thonje ndi barele zinayoyoka; pakuti barele lidafula, ndi thonje lidayamba maluwa.


Mwana wanzeru amamvera mwambo wa atate; koma wonyoza samvera chidzudzulo.


Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru: koma mnzao wa opusa adzaphwetekedwa.


Ndipo pamene Petro anali pansi m'bwalo, anadzapo mmodzi wa adzakazi a mkulu wa ansembe;


Musanyengedwe; mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.


Mudziwerengere masabata asanu ndi awiri; muyambe kuwerenga masabata asanu ndi awiri poyambira kusenga tirigu wachilili.


Momwemo anabwera Naomi ndi Rute Mmowabu mpongozi wake pamodzi naye, amene anabwera kuchokera ku dziko la Mowabu; ndipo anafika ku Betelehemu, pakuyamba anthu kucheka barele.


Nati Naomi kwa Rute mpongozi wake, Nchabwino, mwana wanga, kuti uzituluka nao adzakazi ake, ndi kuti asakukomane m'munda wina uliwonse.


Pamenepo Naomi mpongozi wake ananena naye, Mwana wanga, kodi ndisakufunire popumulako, kuti ukhale bwino?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa