Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Amosi 4:9 - Buku Lopatulika

9 Ndinakukanthani ndi chinsikwi ndi chinoni; minda yanu yochuluka yamipesa, ndi yamikuyu, ndi ya azitona, yaonongeka ndi dzombe; koma simunabwerere kudza kwa Ine, ati Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndinakukanthani ndi chinsikwi ndi chinoni; minda yanu yochuluka yamipesa, ndi yamikuyu, ndi ya azitona, yaonongeka ndi dzombe; koma simunabwerera kudza kwa Ine, ati Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 “Ndidaumitsa mbeu zanu ndi matenda ndiponso ndi chinoni. Chidafotetsa mbeu za m'minda yanu yonse ndi yamphesa yomwe. Dzombe lidaononga mikuyu yanu ndi mitengo ya olivi, komabe simudabwerere kwa Ine.” Akutero Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 “Nthawi zambiri ndinakantha mbewu zanu ndiponso minda ya mpesa, ndinayikantha ndi chinsikwi ndiponso ndi chiwawu. Dzombe linawononga mikuyu yanu ndi mitengo ya olivi. Komabe inu simunabwerere kwa Ine,” akutero Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Amosi 4:9
21 Mawu Ofanana  

M'dziko mukakhala njala, mukakhala mliri, mlaza, chinoni, dzombe, kapena kapuchi, adani ao akawamangira misasa m'dziko la mizinda yao, mukakhala mliri uliwonse, kapena nthenda;


Mukakhala njala m'dzikomo, mukakhala mliri, mukakhala chinsikwi, kapena chinoni, dzombe, kapena kapuche; akawamangira misasa adani ao, m'dziko la mizinda yao; mukakhala mliri uliwonse, kapena nthenda iliyonse;


Nanga bwanji mukali chimenyedwere kuti inu mulikupandukirabe? Mutu wonse ulikudwala, ndi mtima wonse walefuka.


Taonani, inu nonse amene muyatsa moto, amene mudzimangira m'chuuno ndi nsakali, yendani inu m'chilangali cha moto wanu, ndi pakati pa nsakali zimene mwaziyatsa. Ichi mudzakhala nacho cha padzanja langa; mudzagona pansi ndi chisoni.


Aramu patsogolo ndi Afilisti pambuyo; ndipo iwo adzadya Israele ndi kukamwa koyasama. Mwa izi zonse mkwiyo wake sunachoke, koma dzanja lake lili chitambasulire.


Ndipo zingakhale zonsezi Yuda mphwake wonyenga sanabwere kwa Ine ndi mtima wake wonse, koma monama, ati Yehova.


Yehova Inu, maso anu sali pachoonadi kodi? Munawapanda iwo, koma sanaphwetekedwe mtima; munawatha iwo, koma akana kudzudzulidwa; alimbitsa nkhope zao koposa mwala; akana kubwera.


Iye sadzabwerera kunka kudziko la Ejipito, koma Asiriya adzakhala mfumu yake, popeza anakana kubwera.


Chosiya chimbalanga, dzombe lidachidya; ndi chosiya dzombe, chirimamine adachidya; ndi chosiya chirimamine, anoni adachidya.


Unaonongadi mpesa wanga, nunyenya mkuyu wanga, nukungudza konse, nuutaya; nthambi zake zasanduka zotumbuluka.


Ndipo ndidzakubwezerani zaka zidazidya dzombe, ndi chirimamine, ndi anoni, ndi chimbalanga, gulu langa lalikulu la nkhondo, limene ndinalitumiza pakati pa inu.


Ndipo Ine ndakupatsaninso mano oyera m'mizinda yanu yonse, ndi kusowa mkate m'malo mwanu monse; koma simunabwerere kudza kwa Ine, ati Yehova.


M'mwemo mizinda iwiri kapena itatu inayenda peyupeyu kumzinda umodzi kukamwa madzi, koma sanakhute; koma simunabwerere kudza kwa Ine, ati Yehova.


Chinkana mkuyu suphuka, kungakhale kulibe zipatso kumpesa; yalephera ntchito ya azitona, ndi m'minda m'mosapatsa chakudya; ndi zoweta zachotsedwa kukhola, palibenso ng'ombe m'makola mwao;


Ndinakukanthani ndi chinsikwi ndi chinoni ndi matalala m'ntchito zonse za manja anu, koma simunabwerere kudza kwa Ine, ati Yehova.


Ndipo ndidzadzudzula zolusa chifukwa cha inu, kuti zisakuonongereni zipatso za nthaka yanu; ngakhale mpesa wanu sudzayoyoka zipatso zake, zosacha m'munda, ati Yehova wa makamu.


Yehova adzakukanthani ndi nthenda yoondetsa ya chifuwa, ndi malungo, ndi chibayo, ndi kutentha thupi, ndi lupanga, chinsikwi ndi chinoni; ndipo zidzakutsatani kufikira mwatayika.


Mitengo yanu yonse ndi zipatso za nthaka yanu zidzakhala zaozao za dzombe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa