Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Amosi 4:10 - Buku Lopatulika

10 Ndinatumiza mliri pakati panu monga mu Ejipito; anyamata anu ndawapha ndi lupanga, ndi kutenga akavalo anu; ndipo ndinakweretsa kununkha kwa chigono chanu kufikitsa kumphuno kwanu; koma simunabwerere kudza kwa Ine, ati Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ndinatumiza mliri pakati panu monga m'Ejipito; anyamata anu ndawapha ndi lupanga, ndi kutenga akavalo anu; ndipo ndinakweretsa kununkha kwa chigono chanu kufikitsa kumphuno kwanu; koma simunabwerera kudza kwa Ine, ati Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 “Ndidakugwetserani miliri yonga ya ku Ejipito ija. Ndidaphetsa achinyamata anu ku nkhondo, ndidapereka akavalo anu kwa adani. Ndidakununkhitsani fungo la mitembo lochokera ku misasa yanu yankhondo. Komabe simudabwerere kwa Ine.” Akutero Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 “Ine ndinabweretsa miliri pakati panu monga ndinachitira ku Igupto. Ndinapha anyamata anu ndi lupanga, ndinapereka akavalo anu kwa adani. Ndinakununkhitsani fungo la mitembo lochokera mʼmisasa yanu ya nkhondo. Komatu inu simunabwerere kwa Ine,” akutero Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Amosi 4:10
42 Mawu Ofanana  

Masiku ao Yehova anayamba kusadza Israele; ndipo Hazaele anawakantha m'malire onse a Israele,


Ndipo mkwiyo wa Yehova unayaka pa Israele, nawapereka m'dzanja la Hazaele mfumu ya Aramu, ndi m'dzanja la Benihadadi mwana wa Hazaele, masiku onsewo.


Koma mfumu ya Aramu sanasiyire Yehowahazi anthu, koma apakavalo makumi asanu, ndi magaleta khumi, ndi oyenda pansi zikwi khumi; popeza mfumu ya Aramu anawaononga, nawayesa ngati fumbi lopondapo.


Nati Hazaele, Muliriranji, mbuye wanga? Nayankha iye, Popeza ndidziwa choipa udzachitira ana a Israele; udzatentha malinga ao ndi moto, nudzapha anyamata ao ndi lupanga, nudzaphwanya makanda ao, nudzang'amba akazi ao okhala ndi pakati.


Koma Yehova analimbitsa mtima wake wa Farao, ndipo anakana kuwaleka amuke.


Ndipo Mose ndi Aroni analowa kwa Farao nanena naye, Atero Yehova, Mulungu wa Ahebri, Ukana kudzichepetsa pamaso panga kufikira liti? Lola anthu anga amuke, akanditumikire;


Ndipo ndidzalimbitsa mtima wake wa Farao kuti awalondole; ndipo ndidzalemekezedwa pa Farao ndi pa nkhondo yake yonse; pamenepo Aejipito adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndipo anachita chomwecho.


ndipo anati, Ngati udzamveratu mau a Yehova, Mulungu wako, ndi kuchita zoona pamaso pake, ndi kutchera khutu pa malamulo ake, ndi kusunga malemba ake onse, za nthenda zonse ndinaziika pa Aejipito sindidzaziika pa iwe nnena imodzi; pakuti Ine Yehova ndine wakuchiritsa iwe.


Pamenepo alembi anati kwa Farao, Chala cha Mulungu ichi; koma mtima wa Farao unalimba, osamvera iwo; monga adalankhula Yehova.


Koma Yehova analimbitsa mtima wa Farao, kuti sanamvere iwo; monga Yehova adalankhula ndi Mose.


Kodi udzikwezanso pa anthu anga, ndi kusawalola amuke?


Ophedwa aonso adzatayidwa kunja, ndipo kununkha kwa mitembo yao kudzamveka, ndipo mapiri adzasungunuka ndi mwazi wao.


Taonani, inu nonse amene muyatsa moto, amene mudzimangira m'chuuno ndi nsakali, yendani inu m'chilangali cha moto wanu, ndi pakati pa nsakali zimene mwaziyatsa. Ichi mudzakhala nacho cha padzanja langa; mudzagona pansi ndi chisoni.


Aramu patsogolo ndi Afilisti pambuyo; ndipo iwo adzadya Israele ndi kukamwa koyasama. Mwa izi zonse mkwiyo wake sunachoke, koma dzanja lake lili chitambasulire.


Koma anthu sanatembenukire kwa Iye amene anawamenya, ngakhale kufuna Yehova wa makamu.


Chifukwa chake Ambuye sadzakondwera ndi anyamata ao, ngakhale kuwachitira chifundo amasiye ao ana ndi akazi; popeza yense ali wodetsa ndi wochimwa, m'kamwa monse mulankhula zopusa. Mwa izi zonse mkwiyo wake sunachoke, koma dzanja lake lili chitambasulire.


chifukwa chake atero Yehova wa makamu, Taonani, ndidzalanga iwo; anyamata adzafa ndi lupanga; ana ao aamuna ndi aakazi adzafa ndi njala;


Ndipo ndidzaika pa iwo mitundu inai, ati Yehova, lupanga lakupha, agalu akung'amba, mbalame za m'mlengalenga, ndi zilombo zapansi, zakulusa ndi kuononga.


Adzafa ndi imfa zanthenda; sadzaliridwa maliro, sadzaikidwa; adzakhala ngati ndowe panthaka; ndipo adzathedwa lupanga, ndi njala; ndipo mitembo yao idzakhala chakudya cha mbalame za kumlengalenga, ndi zilombo za dziko lapansi.


Chifukwa chake mupereke ana ao kunjala, mupereke iwo kumphamvu ya lupanga; akazi ao akhale opanda ana, ndi amasiye; amuna ao aphedwe ndi imfa, ndi anyamata ao apandidwe ndi lupanga kunkhondo.


Mowabu wapasuka, akwera kulowa m'mizinda yake, ndi anyamata ake osankhika atsikira kukaphedwa, ati Mfumu, dzina lake ndiye Yehova wa makamu.


Chifukwa chake anyamata ake adzagwa m'miseu yake, ndipo anthu onse a nkhondo adzatontholetsedwa tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu.


Yehova Inu, maso anu sali pachoonadi kodi? Munawapanda iwo, koma sanaphwetekedwe mtima; munawatha iwo, koma akana kudzudzulidwa; alimbitsa nkhope zao koposa mwala; akana kubwera.


Chifukwa chake ndadzala ndi ukali wa Yehova; ndalema ndi kudzikaniza; tsanulirani pa ana a pabwalo, ndi pa misonkhano ya anyamata, pakuti ngakhale mwamuna ndi mkazi wake adzatengedwa, okalamba ndi iye amene achuluka masiku ake.


Nenani, atero Yehova, Mitembo yathu idzagwa ngati ndowe pamunda, ndi monga chipukutu pambuyo pa wakusenga, palibe wochitola.


Iye sadzabwerera kunka kudziko la Ejipito, koma Asiriya adzakhala mfumu yake, popeza anakana kubwera.


koma ndidzakuchotserani kutali nkhondo ya kumpoto, ndi kulingira kudziko louma ndi lopasuka, a kumaso kwake kunyanja ya kum'mawa, ndi a kumbuyo kwake kunyanja ya kumadzulo; ndi kununkha kwake kudzakwera, ndi fungo lake loipa lidzakwera; pakuti inachita zazikulu.


ndidzachitira inu ichinso; ndidzakuikirani zoopsa, nthenda yoondetsa ya m'chifuwa ndi malungo, zakulanda maso ndi mphamvu, ndi kuzunza moyo; ndipo mudzabzala mbeu zanu chabe, popeza adani anu adzazidya.


Ndipo ndidzadzetsa kwa inu lupanga lakuchita chilango cha chipangano; kotero kuti mudzasonkhanidwa m'mizinda mwanu; ndipo ndidzatumiza mliri pakati pa inu; ndipo mudzaperekedwa m'manja mwa mdani.


Ndipo Ine ndakupatsaninso mano oyera m'mizinda yanu yonse, ndi kusowa mkate m'malo mwanu monse; koma simunabwerere kudza kwa Ine, ati Yehova.


Koma nyimbo za ku Kachisi zidzasanduka kubuma tsiku ilo, ati Ambuye Yehova; mitembo idzachuluka; adzaitaya paliponse padzakhala zii.


Ndinakukanthani ndi chinsikwi ndi chinoni ndi matalala m'ntchito zonse za manja anu, koma simunabwerere kudza kwa Ine, ati Yehova.


Yehova adzakumamatiritsani mliri, kufikira akakuthani kukuchotsani kudziko, kumene mupitako kulilandira.


Yehova adzakukanthani ndi nthenda yoondetsa ya chifuwa, ndi malungo, ndi chibayo, ndi kutentha thupi, ndi lupanga, chinsikwi ndi chinoni; ndipo zidzakutsatani kufikira mwatayika.


Ndipo adzakubwezerani nthenda zonse za Ejipito, zimene munaziopa; ndipo zidzakumamatirani inu.


Ndipo Yehova adzakuchotserani nthenda zonse; sadzakuikirani nthenda zoipa zilizonse za Aejipito muzidziwa zija; koma adzaziika pa onse akudana ndi inu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa