Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Amosi 4:11 - Buku Lopatulika

11 Ndinagubuduza ena mwa inu, monga umo Mulungu anagubuduzira Sodomu ndi Gomora; ndipo inu munali ngati muuni wofumulidwa kumoto; koma simunabwerere kudza kwa Ine, ati Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndinagubuduza ena mwa inu, monga umo Mulungu anagubuduzira Sodomu ndi Gomora; ndipo inu munali ngati muuni wofumulidwa kumoto; koma simunabwerera kudza kwa Ine, ati Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 “Ndidaononga ena mwa inu, monga momwe ndidaonongera Sodomu ndi Gomora. Otsaliranu munali ngati zikuni zofumula pa moto. Komabe simudabwerere kwa Ine.” Akutero Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 “Ndinawononga ena mwa inu monga ndinawonongera Sodomu ndi Gomora. Inu munali ngati chikuni choyaka chimene chafumulidwa pa moto. Komabe inu simunabwerere kwa Ine,” akutero Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Amosi 4:11
24 Mawu Ofanana  

Ndipo Babiloni, ulemerero wa maufumu, mudzi wokongolawo Ababiloni anaunyadira, adzakhala monga momwe Mulungu anapasula Sodomu ndi Gomora.


nukati kwa iye, Chenjera, khala ulipo; usaope, mtima wako usalefuke, chifukwa cha zidutswa ziwirizi za miuni yofuka, chifukwa cha mkwiyo waukali wa Rezini ndi Aramu, ndi wa mwana wa Remaliya.


Aramu patsogolo ndi Afilisti pambuyo; ndipo iwo adzadya Israele ndi kukamwa koyasama. Mwa izi zonse mkwiyo wake sunachoke, koma dzanja lake lili chitambasulire.


Mwa aneneri a ku Yerusalemu ndinaona chinthu choopsetsa; achita chigololo, ayenda monama, alimbitsa manja a ochita zoipa, ndipo palibe wobwerera kuleka zoipa zake; onse akhala kwa Ine ngati Sodomu, ndi okhalamo ake ngati Gomora.


Monga m'kupasuka kwa Sodomu ndi Gomora ndi mizinda inzake, ati Yehova, munthu aliyense sadzakhala m'menemo, mwana wa munthu aliyense sadzagona m'menemo.


Yehova Inu, maso anu sali pachoonadi kodi? Munawapanda iwo, koma sanaphwetekedwe mtima; munawatha iwo, koma akana kudzudzulidwa; alimbitsa nkhope zao koposa mwala; akana kubwera.


Monga muja Mulungu anagwetsa Sodomu ndi Gomora ndi mizinda inzake, ati Yehova; anthu sadzakhalamo, mwana wa munthu sadzagonamo.


M'chodetsa chako muli dama, popeza ndinakuyeretsa; koma sunayeretsedwa, sudzayeretsedwanso kukuchotsera chodetsa chako, mpaka nditakwaniritsa ukali wanga pa iwe.


Iye sadzabwerera kunka kudziko la Ejipito, koma Asiriya adzakhala mfumu yake, popeza anakana kubwera.


Ndidzakusiya bwanji, Efuremu? Ndidzakupereka bwanji, Israele? Ndidzakuyesa bwanji ngati Adima? Ndidzakuika bwanji ngati Zeboimu? Mtima wanga watembenuka m'kati mwanga, zachifundo zanga zilira zonse pamodzi.


Ndipo Ine ndakupatsaninso mano oyera m'mizinda yanu yonse, ndi kusowa mkate m'malo mwanu monse; koma simunabwerere kudza kwa Ine, ati Yehova.


Ndinakukanthani ndi chinsikwi ndi chinoni ndi matalala m'ntchito zonse za manja anu, koma simunabwerere kudza kwa Ine, ati Yehova.


Ndipo Yehova anati kwa Satana, Yehova akudzudzula, Satana iwe; inde Yehova amene anasankha Yerusalemu akudzudzula; uyu sindiye muuni wofumulidwa kumoto?


Ndipo monga Yesaya anati kale, Ngati Ambuye wa makamu a kumwamba sanatisiyire ife mbeu, tikadakhala monga Sodomu, ndipo tikadafanana ndi Gomora.


Ngati ntchito ya wina itenthedwa, zidzaonongeka zake; koma iye yekha adzapulumutsidwa; koma monga momwe mwa moto.


Yehova adzasanduliza mvula ya dziko lanu ikhale fumbi ndi phulusa; zidzakutsikirani kuchokera kumwamba, kufikira mwaonongeka.


Ndi kuti lidapsa dziko lake lonse ndi sulufure, ndi mchere, kuti sabzalamo, kapena siliphukitsa kanthu kapena sumerapo msipu, monga kupasula kwake kwa Sodomu ndi Gomora, Adima, ndi Zeboimu, imene Yehova anaipasula m'mkwiyo wake ndi ukali wake;


ndipo pakuisandutsa makala mizinda ya Sodomu ndi Gomora anaitsutsa poigwetsa, ataiika chitsanzo cha kwa iwo akakhala osapembedza;


koma ena muwapulumutse ndi kuwakwatula kumoto; koma ena muwachitire chifundo ndi mantha, nimudane naonso malaya ochitidwa mawanga ndi thupi.


Monga Sodomu ndi Gomora, ndi mizinda yakuizungulira, potsatana nayoyo, idadzipereka kudama, ndi kutsata zilakolako zachilendo, iikidwa chitsanzo, pakuchitidwa chilango cha moto wosatha.


Ndipo otsala a anthu osaphedwa nayo miliri iyo sanalape ntchito ya manja ao, kuti asapembedzere ziwanda, ndi mafano agolide, ndi asiliva, ndi amkuwa, ndi a mwala, ndi amtengo, amene sangathe kupenya, kapena kumva, kapena kuyenda;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa