Eksodo 9:19 - Buku Lopatulika Ndipo tsopano, tumiza, thawitsa zoweta zako ndi zonse uli nazo pabwalo; pakuti anthu onse ndi zoweta zonse zopezeka pabwalo, zosasonkhanidwa m'nyumba, matalala adzazigwera, ndipo zidzafa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo tsopano, tumiza, thawitsa zoweta zako ndi zonse uli nazo pabwalo; pakuti anthu onse ndi zoweta zonse zopezeka pabwalo, zosasonkhanidwa m'nyumba, matalala adzazigwera, ndipo zidzafa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsopano lamula kuti zoŵeta zanu zonse zikhale m'khola pamodzi ndi zonse zimene muli nazo. Matalala adzagwa pa anthu ndi pa nyama zonse zongoyenda pa bwalo, chifukwa chosaziloŵetsa m'khola, ndipo zonsezo zidzafa.’ ” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsopano lamula kuti ziweto zanu zonse ndi zinthu zonse zomwe zili ku minda kuti zilowetsedwe mʼkhola, chifukwa matalala adzagwera munthu aliyense ndi chiweto chilichonse chimene sichidzalowetsedwa mʼkhola ndipo zimene zidzakhala zili ku munda zidzafa.” |
Ndipo matalala anapanda m'dziko lonse la Ejipito zonse za pabwalo, kuyambira anthu kufikira zoweta; ndipo matalala anapanda zitsamba zonse zakuthengo, nathyola mitengo yonse yakuthengo.
Ndipo m'mawa mwake Yehova anachita chinthucho, ndipo zinafa zoweta zonse za mu Ejipito; koma sichinafe chimodzi chonse cha zoweta za ana a Israele.
Anamva mau a lipenga, osawalabadira, wadziphetsa ndi mtima wake; akadalabadira, akadalanditsa moyo wake.
Yehova, ndinamva mbiri yanu ndi mantha; Yehova, tsitsimutsani ntchito yanu pakati pa zaka, pakati pa zaka mudziwitse; pa mkwiyo mukumbukire chifundo.