Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 9:25 - Buku Lopatulika

25 Ndipo matalala anapanda m'dziko lonse la Ejipito zonse za pabwalo, kuyambira anthu kufikira zoweta; ndipo matalala anapanda zitsamba zonse zakuthengo, nathyola mitengo yonse yakuthengo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 Ndipo matalala anapanda m'dziko lonse la Ejipito zonse za pabwalo, kuyambira anthu kufikira zoweta; ndipo matalala anapanda zitsamba zonse za kuthengo, nathyola mitengo yonse ya kuthengo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 Matalalawo adaononga zonse zokhala panja m'dziko lonse la Ejipito, anthu onse pamodzi ndi nyama zomwe. Adaononganso zomera zonse zam'minda ndi kukadzulanso mitengo yonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 Matalala anawononga dziko lonse la Igupto, munthu aliyense pamodzi ndi ziweto. Matalala aja anawononga zomera zonse za mʼmunda ndi kukhadzula mtengo uliwonse.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 9:25
8 Mawu Ofanana  

Anapha mphesa zao ndi matalala, ndi mikuyu yao ndi chisanu.


Naperekanso zoweta zao kwa matalala, ndi ng'ombe zao kwa mphezi.


Ndipo tsopano, tumiza, thawitsa zoweta zako ndi zonse uli nazo pabwalo; pakuti anthu onse ndi zoweta zonse zopezeka pabwalo, zosasonkhanidwa m'nyumba, matalala adzazigwera, ndipo zidzafa.


Potero panali matalala, ndi moto wakutsikatsika pakati pa matalala, choopsa ndithu; panalibe chotere m'dziko lonse la Ejipito chiyambire mtundu wao.


Ndipo m'mawa mwake Yehova anachita chinthucho, ndipo zinafa zoweta zonse za mu Ejipito; koma sichinafe chimodzi chonse cha zoweta za ana a Israele.


Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Ndidzalithithimula ndi mkuntho mu ukali wanga; ndipo lidzavumbidwa ndi mvula yaikulu mu mkwiyo wanga, ndi matalala aakulu adzalitha mu ukali wanga.


Ndipo kunali, pakuthawa iwo pamaso pa Israele, potsikira pa Betehoroni, Yehova anawagwetsera miyala yaikulu yochokera kumwamba mpaka pa Azeka, nafa iwo; akufa ndi miyala yamatalala anachuluka ndi iwo amene ana a Israele anawapha ndi lupanga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa