Ndipo Yehova anati kwa Mose, Lowa kwa Farao; pakuti ndaumitsa mtima wake, ndi mtima wa anyamata ake, kuti ndiike zizindikiro zanga izi pakati pao;
Eksodo 9:12 - Buku Lopatulika Koma Yehova analimbitsa mtima wa Farao, kuti sanamvere iwo; monga Yehova adalankhula ndi Mose. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Yehova analimbitsa mtima wa Farao, kuti sanamvere iwo; monga Yehova adalankhula ndi Mose. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Mulungu adamuumitsa mtima Farao, ndipo Faraoyo sadaŵalole anthuwo kuti apite monga momwe Chauta adaauzira Mose muja. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma Yehova anawumitsa mtima wa Farao ndipo iye sanamvere Mose ndi Aaroni monga momwe Yehova anamuwuzira Mose. |
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Lowa kwa Farao; pakuti ndaumitsa mtima wake, ndi mtima wa anyamata ake, kuti ndiike zizindikiro zanga izi pakati pao;
Ndipo Mose ndi Aroni anachita zozizwa izi zonse pamaso pa Farao; koma Yehova analimbitsa mtima wake wa Farao, ndipo sanalole ana a Israele atuluke m'dziko lake.
Ndipo Yehova analimbitsa mtima wa Farao, mfumu ya Aejipito, ndipo iye analondola ana a Israele; koma ana a Israele adatuluka ndi dzanja lokwezeka.
Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Pakumuka iwe kubwerera kunka ku Ejipito, usamalire uchite zozizwa zonse ndaziika m'dzanja lako, pamaso pa Farao; koma Ine ndidzalimbitsa mtima wake kuti asadzalole anthu kupita.
Koma Farao sadzamvera inu, ndipo ndidzaika dzanja langa pa Aejipito, ndipo ndidzatulutsa makamu anga, anthu anga ana a Israele, m'dziko la Ejipito ndi maweruzo aakulu.
Ndipo Farao anatuma, taonani, sichidafe chingakhale chimodzi chomwe cha zoweta za Aisraele. Koma mtima wa Farao unauma, ndipo sanalole anthu amuke.
Wadetsa maso ao, naumitsa mtima wao; kuti angaone ndi maso, angazindikire ndi mtima, nangatembenuke, ndipo ndingawachiritse.
Pakuti chidadzera kwa Yehova kulimbitsa mitima yao kuti athirane nao Aisraele nkhondo kuti Iye awaononge konse, kuti asawachitire chifundo koma awaononge, monga Yehova adalamulira Mose.