Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 11:10 - Buku Lopatulika

10 Ndipo Mose ndi Aroni anachita zozizwa izi zonse pamaso pa Farao; koma Yehova analimbitsa mtima wake wa Farao, ndipo sanalole ana a Israele atuluke m'dziko lake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ndipo Mose ndi Aroni anachita zozizwa izi zonse pamaso pa Farao; koma Yehova analimbitsa mtima wake wa Farao, ndipo sanalole ana a Israele atuluke m'dziko lake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Motero Mose ndi Aroni adachita zozizwitsa zonsezi pamaso pa Farao. Koma Chauta adamuumitsa mtima Faraoyo, ndipo Aisraelewo sadaŵalole kuti achoke m'dziko mwake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Mose ndi Aaroni anachita zodabwitsa zonsezi pamaso pa Farao koma Yehova anawumitsa mtima wa Farao, ndipo sanalole kuti Aisraeli atuluke mʼdziko lake.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 11:10
17 Mawu Ofanana  

Ndiye wa mtima wanzeru, ndi wa mphamvu yaikulu; ndaniyo anadziumitsa mtima pa Iye, nakhala nao mtendere?


Koma Yehova analimbitsa mtima wa Farao, ndipo sanalole ana a Israele amuke.


Koma Yehova analimbitsa mtima wake wa Farao, ndipo anakana kuwaleka amuke.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni m'dziko la Ejipito, ndi kuti,


Koma Ine ndidziwa kuti mfumu ya Aejipito siidzalola inu kumuka, inde lingakhale ndi dzanja lamphamvu ai.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Pakumuka iwe kubwerera kunka ku Ejipito, usamalire uchite zozizwa zonse ndaziika m'dzanja lako, pamaso pa Farao; koma Ine ndidzalimbitsa mtima wake kuti asadzalole anthu kupita.


Koma Ine ndidzaumitsa mtima wake wa Farao, ndipo ndidzachulukitsa zizindikiro ndi zozizwa zanga m'dziko la Ejipito.


Koma Yehova analimbitsa mtima wa Farao, kuti sanamvere iwo; monga Yehova adalankhula ndi Mose.


Yehova bwanji mwatisocheretsa kusiya njira zanu, ndi kuumitsa mitima yathu tisakuopeni? Bwerani, chifukwa cha atumiki anu, mafuko a cholowa chanu.


Wadetsa maso ao, naumitsa mtima wao; kuti angaone ndi maso, angazindikire ndi mtima, nangatembenuke, ndipo ndingawachiritse.


Chotero Iye achitira chifundo amene Iye afuna, ndipo amene Iye afuna amuumitsa mtima.


Ndipo titani ngati Mulungu, pofuna Iye kuonetsa mkwiyo wake, ndi kudziwitsa mphamvu yake, analekerera ndi chilekerero chambiri zotengera za mkwiyo zokonzekera chionongeko?


Koma Sihoni mfumu ya Hesiboni sanatilole kupitira kwao; popeza Yehova Mulungu wanu anaumitsa mzimu wake, nalimbitsa mtima wake, kuti ampereke m'dzanja lanu, monga lero lino.


Pakuti chidadzera kwa Yehova kulimbitsa mitima yao kuti athirane nao Aisraele nkhondo kuti Iye awaononge konse, kuti asawachitire chifundo koma awaononge, monga Yehova adalamulira Mose.


Mulikuumitsiranji mitima yanu, monga Aejipito ndi Farao anaumitsa mitima yao? Kodi iwo sanalole anthuwo amuke, Iye atachita kodabwitsa pakati pao, ndipo anamuka?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa