Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Pakumuka iwe kubwerera kunka ku Ejipito, usamalire uchite zozizwa zonse ndaziika m'dzanja lako, pamaso pa Farao; koma Ine ndidzalimbitsa mtima wake kuti asadzalole anthu kupita.
Eksodo 8:32 - Buku Lopatulika Koma Farao anaumitsa mtima wake nthawi yomweyonso, ndipo sanalole anthu amuke. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Farao anaumitsa mtima wake nthawi yomweyonso, ndipo sanalola anthu amuke. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma ngakhale pa nthaŵi imeneyinso, Farao adakhala wokanikabe, ndipo sadalole kuti Aisraele apite. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma nthawi imeneyinso Farao anawumitsa mtima wake ndipo sanalole kuti anthu atuluke. |
Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Pakumuka iwe kubwerera kunka ku Ejipito, usamalire uchite zozizwa zonse ndaziika m'dzanja lako, pamaso pa Farao; koma Ine ndidzalimbitsa mtima wake kuti asadzalole anthu kupita.
Koma pamene Farao anaona kuti panali kupuma, anaumitsa mtima wake, osamvera iwo; monga adalankhula Yehova.
Ndipo Yehova anachita monga mwa mau a Mose; nachotsera Farao ndi anyamata ake ndi anthu ake mizazayo, sunatsale ndi umodzi wonse.
Pamenepo Farao anaitana Mose ndi Aroni, nati, Mundipembere Yehova, kuti andichotsere ine ndi anthu anga achulewo; ndipo ndidzalola anthu amuke, kuti amphere Yehova nsembe.
Ndipo Farao anatuma, taonani, sichidafe chingakhale chimodzi chomwe cha zoweta za Aisraele. Koma mtima wa Farao unauma, ndipo sanalole anthu amuke.
Yehova bwanji mwatisocheretsa kusiya njira zanu, ndi kuumitsa mitima yathu tisakuopeni? Bwerani, chifukwa cha atumiki anu, mafuko a cholowa chanu.
Koma kolingana ndi kuuma kwako, ndi mtima wako wosalapa, ulikudziunjikira wekha mkwiyo pa tsiku la mkwiyo ndi la kuvumbulutsa kuweruza kolungama kwa Mulungu;
Mulikuumitsiranji mitima yanu, monga Aejipito ndi Farao anaumitsa mitima yao? Kodi iwo sanalole anthuwo amuke, Iye atachita kodabwitsa pakati pao, ndipo anamuka?