Eksodo 8:3 - Buku Lopatulika
ndipo m'mtsinjemo mudzachuluka achule, amene adzakwera nadzalowa m'nyumba mwako, ndi m'chipinda chogona iwe, ndi pakama pako, ndi m'nyumba ya anyamata ako, ndi pa anthu ako, m'michembo yanu yootcheramo, ndi m'mbale zanu zoumbiramo.
Onani mutuwo
ndipo m'nyanjamo mudzachuluka achule, amene adzakwera nadzalowa m'nyumba mwako, ndi m'chipinda chogona iwe, ndi pakama pako, ndi m'nyumba ya anyamata ako, ndi pa anthu ako, m'michembo yanu yoocheramo, ndi m'mbale zanu zoumbiramo.
Onani mutuwo
Mtsinje uja udzakhala wodzaza ndi achule. Adzachokera mumtsinjemo namakaloŵa m'chipinda mwako mogona, pabedi pako, m'nyumba za nduna zako ndi za anthu ako, m'malo onse ophikira ndi mophikira buledi momwe.
Onani mutuwo
Mtsinje wa Nailo udzadzaza ndi achule. Achulewo adzatuluka ndi kukalowa mʼnyumba yaufumu, ku chipinda chogona ndi pa bedi lako, mʼnyumba za nduna zako ndi pa anthu ako ndi mophikira buledi ndiponso mopangira bulediyo.
Onani mutuwo