Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 12:34 - Buku Lopatulika

34 Ndipo anthu anatenga mtanda wao usanatupe, ndi zoumbiramo zao zomangidwa m'zovala zao pa mapewa ao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

34 Ndipo anthu anatenga mtanda wao usanatupe, ndi zoumbiramo zao zomangidwa m'zovala zao pa mapewa ao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

34 Motero anthuwo adanyamula pa mapewa ao ufa wa buledi wokandiratu asanathire chofufumitsira, pamodzi ndi mbale zokandiramo buledi zili zokulunga m'nsalu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

34 Motero anthuwo ananyamula ufa wawo wopangira buledi asanathiremo yisiti ndipo anasenza pa mapewa awo pamodzi ndi zokandiramo buledi atazikulunga mu nsalu.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 12:34
3 Mawu Ofanana  

Ndipo anaotcha timitanda topanda chotupitsa ta mtanda umene anabwera nao ku Ejipito, popeza sadaikamo chotupitsa; pakuti adawapirikitsa ku Ejipito, ndipo sanathe kuchedwa, kapena kudzikonzeratu kamba.


ndipo m'mtsinjemo mudzachuluka achule, amene adzakwera nadzalowa m'nyumba mwako, ndi m'chipinda chogona iwe, ndi pakama pako, ndi m'nyumba ya anyamata ako, ndi pa anthu ako, m'michembo yanu yootcheramo, ndi m'mbale zanu zoumbiramo.


Fanizo lina ananena kwa iwo; Ufumu wa Kumwamba uli wofanafana ndi chotupitsa mikate, chimene mkazi anachitenga, nachibisa m'miyeso itatu ya ufa, kufikira wonse unatupa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa