Ndipo Elisa anati, Mverani mau a Yehova; atero Yehova, Mawa dzuwa lino adzagula muyeso wa ufa ndi sekeli, adzagulanso miyeso iwiri ya barele ndi sekeli, pa chipata cha Samariya.
Eksodo 8:23 - Buku Lopatulika Ndipo ndidzaika chosiyanitsa pakati pa anthu anga ndi anthu ako; mawa padzakhala chizindikiro ichi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ndidzaika chosiyanitsa pakati pa anthu anga ndi anthu ako; mawa padzakhala chizindikiro ichi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndidzasiyanitsa ndithu pakati pa anthu anga ndi anthu ako. Chozizwitsa chimenechi chichitika maŵali.’ ” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndidzasiyanitsa pakati pa anthu anga ndi anthu ako. Chizindikiro chozizwitsa ichi chidzachitika mawa.” |
Ndipo Elisa anati, Mverani mau a Yehova; atero Yehova, Mawa dzuwa lino adzagula muyeso wa ufa ndi sekeli, adzagulanso miyeso iwiri ya barele ndi sekeli, pa chipata cha Samariya.
Ndipo adzamvera mau ako; ndipo ukapite iwe ndi akulu a Israele, kwa mfumu ya Aejipito, ndi kukanena naye, Yehova, Mulungu wa Ahebri wakomana ndi ife; tiloleni, timuke tsopano ulendo wa masiku atatu m'chipululu, kuti timphere nsembe Yehova Mulungu wathu.
Ndipo tsiku ilo ndidzalemba malire dziko la Goseni, m'mene mukhala anthu anga, kuti pamenepo pasakhale mizaza; kotero kuti udziwe kuti Ine ndine Yehova pakati padzikoli.
Ndipo Yehova anachita chomwecho; ndipo kunafika magulu a mizaza m'nyumba ya Farao, ndi m'nyumba za anyamata ake, ndi m'dziko lonse la Ejipito; dziko linaipatu chifukwa cha mizazayo.