Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 8:24 - Buku Lopatulika

24 Ndipo Yehova anachita chomwecho; ndipo kunafika magulu a mizaza m'nyumba ya Farao, ndi m'nyumba za anyamata ake, ndi m'dziko lonse la Ejipito; dziko linaipatu chifukwa cha mizazayo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 Ndipo Yehova anachita chomwecho; ndipo kunafika magulu a mizaza m'nyumba ya Farao, ndi m'nyumba za anyamata ake, ndi m'dziko lonse la Ejipito; dziko linaipatu chifukwa cha mizazayo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 Choncho Chauta adachitadi zimenezi, ndipo magulu a mizaza adaloŵa m'nyumba ya Farao, m'nyumba za nduna zake, ndiponso m'dziko lonse la Ejipito. Dziko lonselo lidaipiratu ndi mizazayo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 Ndipo Yehova anachita zimenezi: Ntchentche zoluma zochuluka zinalowa mʼnyumba yaufumu ya Farao ndi nyumba za nduna zake. Choncho ntchentche zolumazi zinawononga dziko lonse la Igupto.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 8:24
6 Mawu Ofanana  

Ananena, ndipo inadza mitambo ya ntchentche, ndi nsabwe kufikira m'malire ao onse.


Anawatumizira pakati pao mitambo ya ntchentche zakuwatha; ndi achule akuwaononga.


Ndipo anawaola miulumiulu; ndi dziko linanunkha.


Pakuti ukapanda kulola anthu anga amuke, taona, ndidzatuma mizaza pa iwe, ndi pa anyamata ako, ndi pa anthu ako, ndi pa nyumba zako; ndipo nyumba za Aejipito zidzadzala nayo mizaza, ndi nthaka yomwe imene ikhalapo.


Ndipo ndidzaika chosiyanitsa pakati pa anthu anga ndi anthu ako; mawa padzakhala chizindikiro ichi.


Ndipo achule adzakwera pa iwe, ndi pa anthu ako, ndi pa anyamata ako onse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa