Pamenepo anati kwa Gehazi, Udzimangire m'chuuno, nutenge ndodo yanga m'dzanja lako, numuke; ukakomana ndi munthu usampatse moni; wina akakupatsa moni usamyankhe; ukaike ndodo yanga pankhope pa mwanayo.
Eksodo 7:20 - Buku Lopatulika Ndipo Mose ndi Aroni anachita monga momwe Yehova adawalamulira; nasamula ndodo, napanda madzi ali m'mtsinjemo pamaso pa Farao, ndi pamaso pa anyamata ake; ndipo madzi onse a m'mtsinjemo anasanduka mwazi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose ndi Aroni anachita monga momwe Yehova adawalamulira; nasamula ndodo, napanda madzi ali m'nyanjamo pamaso pa Farao, ndi pamaso pa anyamata ake; ndipo madzi onse a m'nyanjamo anasanduka mwazi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Motero Mose ndi Aroni adachita monga momwe Chauta adaŵalamulira. Aroni adasamula ndodo yake namenya madzi amumtsinje pamaso pa Farao ndi nduna zake, ndipo madzi onsewo adasanduka magazi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mose ndi Aaroni anachita monga momwe Yehova analamulira. Anakweza ndodo yake pamaso pa Farao ndi akuluakulu ake ndipo anamenya madzi a mu Nailo, ndipo madzi onse anasanduka magazi. |
Pamenepo anati kwa Gehazi, Udzimangire m'chuuno, nutenge ndodo yanga m'dzanja lako, numuke; ukakomana ndi munthu usampatse moni; wina akakupatsa moni usamyankhe; ukaike ndodo yanga pankhope pa mwanayo.
Ndipo kudzatero, akapanda kukhulupirira zingakhale zizindikiro izi, ndi kusamvera mau ako, ukatunge madzi a kumtsinje ndi kuthira pamtunda; ndi madzi watunga ku mtsinjewo adzasanduka mwazi pamtunda.
Ndipo Mose ndi Aroni analowa kwa Farao, nachita monga momwe Yehova adawalamulira; ndipo Aroni anaponya pansi ndodo yake pamaso pa Farao, ndi pamaso pa anyamata ake, ndipo inasanduka chinjoka.
Ndi nsomba za m'mtsinjemo zinafa; ndi mtsinjewo unanunkha; ndipo Aejipito sanakhoze kumwa madzi a m'mtsinjemo; ndipo munali mwazi m'dziko lonse la Ejipito.
Kodi Yehova anaipidwa nayo mitsinje? Mkwiyo wanu unali pamitsinje kodi, kapena ukali wanu panyanja, kuti munayenda pa akavalo anu, pa magaleta anu a chipulumutso?
Ndipo mngelo wachiwiri anaomba lipenga, ndipo monga ngati phiri lalikulu lakupserera ndi moto linaponyedwa m'nyanja; ndipo limodzi la magawo atatu a nyanja linasanduka mwazi;