Eksodo 7:2 - Buku Lopatulika Iwe uzilankhula zonse ndikulamulira; ndi Aroni mkulu wako azilankhula kwa Farao, kuti alole ana a Israele atuluke m'dziko lake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Iwe uzilankhula zonse ndikulamulira; ndi Aroni mkulu wako azilankhula kwa Farao, kuti alole ana a Israele atuluke m'dziko lake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zonse zimene ndakulamulazi ukazinene, ndipo iye ndiye akauze Farao kuti aŵalole Aisraele kutuluka m'dziko mwake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwe ukanene zonse zimene ndakulamulirazi, ndipo Aaroni mʼbale wako ndiye akaziyankhule kwa Farao kuti atulutse ana a Israeli mʼdziko la Igupto. |
Ndipo ukalankhule naye, ndi kumpangira mau; ndipo Ine ndidzakhala m'kamwa mwako, ndi m'kamwa mwake, ndipo ndidzakuphunzitsani inu chimene mukachite.
Ndipo iye adzakulankhulira iwe kwa anthu; ndipo kudzatero, kuti iye adzakhala kwa iwe ngati m'kamwa, ndi iwe udzakhala kwa iye ngati Mulungu.
Ndipo pambuyo pake Mose ndi Aroni analowa nanena ndi Farao, Atero Yehova, Mulungu wa Israele, Lola anthu anga apite, kundichitira madyerero m'chipululu.
Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, Ine ndine Yehova; lankhula ndi Farao mfumu ya Aejipito zonsezi Ine ndizinena nawe.
Koma iwe ukwinde m'chuuno mwako, nuuke, nunene kwa iwo zonse zimene ndikuuza iwe; usaope nkhope zao ndingakuopetse iwe pamaso pao.
Koma Yehova anati kwa ine, Usati, ndine mwana pakuti udzanka kwa yense amene ndidzakutumako iwe, nudzanena chonse chimene ndidzakuuza.
Ananenanso nane, Wobadwa ndi munthu iwe, mau anga onse ndidzawanena ndi iwe uwalandire m'mtima mwako, utawamva m'makutu mwako.
Wobadwa ndi munthu iwe, ndakuika ukhale mlonda wa nyumba ya Israele, m'mwemo mvera mau otuluka m'kamwa mwanga, nundichenjezere iwo.
ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.
Musamaonjeza pa mau amene ndikuuzani, kapena kuchotsapo, kuti musunge malamulo a Yehova Mulungu wanu, amene ndikuuzani.