Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 7:2 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Iwe ukanene zonse zimene ndakulamulirazi, ndipo Aaroni mʼbale wako ndiye akaziyankhule kwa Farao kuti atulutse ana a Israeli mʼdziko la Igupto.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

2 Iwe uzilankhula zonse ndikulamulira; ndi Aroni mkulu wako azilankhula kwa Farao, kuti alole ana a Israele atuluke m'dziko lake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Iwe uzilankhula zonse ndikulamulira; ndi Aroni mkulu wako azilankhula kwa Farao, kuti alole ana a Israele atuluke m'dziko lake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Zonse zimene ndakulamulazi ukazinene, ndipo iye ndiye akauze Farao kuti aŵalole Aisraele kutuluka m'dziko mwake.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 7:2
13 Mawu Ofanana  

Koma Mikaya anati, “Pali Yehova wamoyo, ine ndikawawuza zokhazo zimene Yehova akandiwuze.”


Iwe udzayankhula naye ndi kumuwuza mawu oti akanene. Ine ndidzakuthandizani kuyankhula nonse awirinu ndi kukulangizani zoti mukachite.


Iye akayankhula kwa anthu mʼmalo mwako. Iye adzakhala wokuyankhulira ndipo iweyo udzakhala ngati Mulungu kwa iye.


Zitachitika izi, Mose ndi Aaroni anapita kwa Farao ndipo anati, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Aloleni anthu anga apite, kuti akachite chikondwerero cha Ine mʼchipululu.’ ”


anati, “Ine ndine Yehova. Umuwuze Farao mfumu ya Igupto zonse zimene Ine ndikuwuze iwe.”


Mose ndi Aaroni anachita monga momwe Yehova anawalamulira.


“Koma iwe Yeremiya konzeka! Nyamuka ndipo ukawawuze zonse zimene ndakulamulira. Usachite nawo mantha, kuopa kuti Ine ndingakuchititse mantha iwo akuona.


Koma Yehova anandiwuza kuti, “Usanene kuti, ‘Ndikanali wamngʼono’ popeza udzapita kwa munthu aliyense kumene ndidzakutuma ndi kunena chilichonse chimene ndidzakulamulira.


Anatinso, “Iwe mwana wa munthu, umvetsetse bwino zimene ndikukuwuzazi ndipo mawu angawa uwasunge bwino mu mtima mwako.


“Iwe mwana wa munthu, Ine ndakuyika kuti ukhale mlonda wa Aisraeli. Uziti ukamva mawu anga, ndiye uzikawachenjeza.


ndi kuwaphunzitsa amvere zonse zimene ndinakulamulirani. Ndipo onani, Ine ndidzakhala pamodzi ndi inu kufikira kutha kwa dziko lapansi pano.”


Pakuti sindinakubisireni pokulalikirani chifuniro chonse cha Mulungu.


Musawonjezere pa zimene ndikukulamulirani ndipo musachotserepo, koma muwasunge malamulo a Yehova Mulungu wanu amene ndikukupatsani.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa