Ndi nsomba za m'mtsinjemo zinafa; ndi mtsinjewo unanunkha; ndipo Aejipito sanakhoze kumwa madzi a m'mtsinjemo; ndipo munali mwazi m'dziko lonse la Ejipito.
Eksodo 7:18 - Buku Lopatulika Ndi nsomba zili m'mtsinje zidzafa, ndi mtsinje idzanunkha; ndi Aejipito adzachita mtima useru ndi kumwa madzi a m'mtsinjemo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndi nsomba zili m'nyanja zidzafa, ndi nyanja idzanunkha; ndi Aejipito adzachita mtima useru ndi kumwa madzi a m'nyanjamo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nsomba zonse zidzafa, ndipo madziwo adzanunkha, kotere kuti Aejipito sadzafunanso kumwa madzi a mu mtsinje umenewu.’ ” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nsomba za mu Nailo zidzafa, mtsinje udzanunkha ndipo Aigupto sadzatha kumwa madzi ake.’ ” |
Ndi nsomba za m'mtsinjemo zinafa; ndi mtsinjewo unanunkha; ndipo Aejipito sanakhoze kumwa madzi a m'mtsinjemo; ndipo munali mwazi m'dziko lonse la Ejipito.
Koma Aejipito onse anakumba m'mphepete mwa mtsinje kufuna madzi akumwa; pakuti sanakhoze kumwa madzi a m'mtsinjemo.
Ndipo timitsinje tidzanunkha; mitsinje ya Ejipito idzachepa, nuima; bango ndi mlulu zidzafota.
koma mwezi wamphumphu, kufikira ibwera m'mphuno mwako, ndi kuti ufukidwa nayo, pakuti mwakaniza Yehova wakukhala pakati pa inu, ndi kulira pamaso pake, ndi kuti, Tinatulukiranji mu Ejipito?
Ndipo anthu ananena motsutsana ndi Mulungu, ndi Mose, ndi kuti, Mwatikwezeranji kutichotsa ku Ejipito kuti tifere m'chipululu? Pakuti mkate ndi madzi palibe, ndi mtima wathu walema nao mkate wachabe uwu.