Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 21:5 - Buku Lopatulika

5 Ndipo anthu ananena motsutsana ndi Mulungu, ndi Mose, ndi kuti, Mwatikwezeranji kutichotsa ku Ejipito kuti tifere m'chipululu? Pakuti mkate ndi madzi palibe, ndi mtima wathu walema nao mkate wachabe uwu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndipo anthu ananena motsutsana ndi Mulungu, ndi Mose, ndi kuti, Mwatikwezeranji kutichotsa ku Ejipito kuti tifere m'chipululu? Pakuti mkate ndi madzi palibe, ndi mtima wathu walema nao mkate wachabe uwu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Anthu aja adayamba kuŵiringulira Mulungu ndiponso Mose, adati, “Chifukwa chiyani mudatitulutsa m'dziko la Ejipito kuti tidzafere m'chipululu muno? Pakuti kuno kulibe ndi chakudya chomwe ngakhalenso madzi, ndipo chakudya chachabechi chatikola.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 ndipo anayankhula motsutsana ndi Mulungu ndi Mose, nati, “Chifukwa chiyani munatitulutsa kuchoka mʼdziko la Igupto kuti tidzafere mʼchipululu muno? Kuno kulibe chakudya, kulibe madzi ndipo chakudya cha chabechabechi tatopa nacho.”

Onani mutuwo Koperani




Numeri 21:5
19 Mawu Ofanana  

Mulungu amangitsira banja anthu a pa okha; atulutsa am'ndende alemerere; koma opikisana naye akhala m'dziko lopanda madzi.


Ndipo analankhula motsutsana ndi Mulungu; anati, Kodi Mulungu akhoza kutikonzera podyera m'chipululu?


Ndipo anati kwa Mose, Kodi mwatichotsera kuti tikafe m'chipululu chifukwa panalibe manda mu Ejipito? Nchiyani ichi mwatichitira kuti mwatitulutsa mu Ejipito?


Ndipo anthu anadandaulira Mose, ndi kuti, Tidzamwa chiyani?


Ndipo pamene ana a Israele anakaona, anati wina ndi mnzake, Nchiyani ichi? Pakuti sanadziwe ngati nchiyani. Ndipo Mose ananena nao, Ndiwo mkatewo Yehova wakupatsani ukhale chakudya chanu.


Ndipo mbumba ya Israele inautcha dzina lake Mana; ndiwo ngati zipatso zampasa, oyera; powalawa akunga timitanda tosakaniza ndi uchi.


Mtima wokhuta upondereza chisa cha uchi; koma wakumva njala ayesa zowawa zonse zotsekemera.


Koma anawo anapandukira Ine, sanayende m'malemba anga, kapena kusunga maweruzo anga kuwachita, amene munthu akawachita adzakhala nao ndi moyo; anaipsa masabata anga; pamenepo ndinati ndidzawatsanulira ukali wanga, kuwakwaniritsira mkwiyo wanga m'chipululu.


koma mwezi wamphumphu, kufikira ibwera m'mphuno mwako, ndi kuti ufukidwa nayo, pakuti mwakaniza Yehova wakukhala pakati pa inu, ndi kulira pamaso pake, ndi kuti, Tinatulukiranji mu Ejipito?


Koma m'mawa mwake khamu lonse la ana a Israele anadandaula pa Mose ndi Aroni, nati, Mwapha anthu a Yehova, inu.


Pamenepo ana a Israele ananena ndi Mose, nati, Taonani, tikufa, tionongeka, tionongeka tonse.


Kapena tisayese Ambuye, monga ena a iwo anayesa, naonongeka ndi njoka zija.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa