mwana wa Abisuwa mwana wa Finehasi, mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni wansembe wamkulu.
Eksodo 6:25 - Buku Lopatulika Ndipo Eleazara mwana wa Aroni anadzitengera mkazi wa ana aakazi a Putiyele akhale mkazi wake, ndipo anambalira Finehasi. Amenewo ndi akulu a makolo a Alevi mwa mabanja ao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Eleazara mwana wa Aroni anadzitengera mkazi wa ana akazi a Putiyele akhale mkazi wake, ndipo anambalira Finehasi. Amenewo ndi akulu a makolo a Alevi mwa mabanja ao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Eleazara mwana wa Aroni adakwatira mmodzi mwa ana a Putiyele, amene adamubalira Finehasi. Ameneŵa ndiwo atsogoleri a mabanja a Alevi malinga ndi mafuko ao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Eliezara mwana wa Aaroni anakwatira mmodzi mwa ana aakazi a Putieli, ndipo anabereka Finehasi. Awa anali atsogoleri a mabanja a Levi, monga mwa mafuko awo. |
mwana wa Abisuwa mwana wa Finehasi, mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni wansembe wamkulu.
Ndipo awa ndi owerengedwa ao a Alevi monga mwa mabanja ao: Geresoni, ndiye kholo la banja la Ageresoni; Kohati, ndiye kholo la banja la Akohati; Merari, ndiye kholo la banja la Amerari.
Ndipo Mose anawatuma a fuko limodzi chikwi chimodzi, kunkhondo, iwowa ndi Finehasi mwana wa Eleazara wansembe, kunkhondo, ndi zipangizo zopatulika, ndi malipenga oliza m'dzanja lake.
Ndipo ana a Israele anatumiza kwa ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi hafu la fuko la Manase, ku dziko la Giliyadi, Finehasi mwana wa Eleazara wansembe,
Eleazaranso mwana wa Aroni anafa; ndipo anamuika paphiri la Finehasi mwana wake, limene adampatsa ku mapiri a Efuremu.
namaima ku likasalo Finehasi mwana wa Eleazara mwana wa Aroni, masiku aja; nati, Kodi nditulukenso kulimbana nkhondo ndi ana a Benjamini mbale wanga, kapena ndileke? Ndipo Yehova anati, Kwerani, pakuti mawa ndidzampereka m'dzanja lako.