Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 31:6 - Buku Lopatulika

6 Ndipo Mose anawatuma a fuko limodzi chikwi chimodzi, kunkhondo, iwowa ndi Finehasi mwana wa Eleazara wansembe, kunkhondo, ndi zipangizo zopatulika, ndi malipenga oliza m'dzanja lake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo Mose anawatuma a fuko limodzi chikwi chimodzi, kunkhondo, iwowa ndi Finehasi mwana wa Eleazara wansembe, kunkhondo, ndi zipangizo zopatulika, ndi malipenga oliza m'dzanja lake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Mose adaŵatumiza ku nkhondo anthuwo, chikwi chimodzi pa fuko lililonse, pamodzi ndi Finehasi mwana wa wansembe Eleazara, iyeyu atanyamula zipangizo za ku malo opatulika ndi malipenga ochenjeza m'manja mwake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Mose anawatumiza ku nkhondo, anthu 1,000 kuchokera ku fuko lililonse pamodzi ndi Finehasi mwana wa Eliezara wansembe amene ananyamula zipangizo zochokera ku malo wopatulika ndi malipenga okaliza.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 31:6
17 Mawu Ofanana  

Uriya nanena ndi Davide, Likasalo, ndi Israele, ndi Yuda, alikukhala m'misasa, ndi mbuye wanga Yowabu, ndi anyamata a mbuye wanga alikugona kuthengo, potero ndikapita ine kodi kunyumba yanga kuti ndidye, ndimwe, ndigone ndi mkazi wanga? Pali inu, pali moyo wanu, sindidzachita chinthuchi.


mwana wa Abisuwa mwana wa Finehasi, mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni wansembe wamkulu.


Monga mwa zonse Ine ndilikuonetsa iwe, chifaniziro cha chihema, ndi chifaniziro cha zipangizo zake zonse, momwemo uchimange.


Koma anakwera pamwamba paphiri modzikuza; koma likasa la chipangano la Yehova, ndi Mose, sanachoke kuchigono.


Ndipo anapereka mwa zikwi za Israele, a fuko limodzi chikwi chimodzi, anthu zikwi khumi ndi ziwiri okonzekeratu ndi zankhondo.


Ndipo kudzali, pamene muyandikiza kunkhondo, ayandikize wansembe nanene ndi anthu,


Ndipo ana a Israele anatumiza kwa ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi hafu la fuko la Manase, ku dziko la Giliyadi, Finehasi mwana wa Eleazara wansembe,


Ndipo Saulo ananena ndi Ahiya, Bwera nalo likasa la Mulungu kuno. Pakuti likasa la Mulungu linali kumeneko masiku aja ndi ana a Israele.


Ndipo Davide anadziwa kuti Saulo analikulingalira zomchitira zoipa; nati kwa Abiyatara wansembe, Bwera kuno ndi efodi.


Ndipo wakubwera ndi mauyo anayankha, nati, Israele anathawa pamaso pa Afilisti, ndiponso kunali kuwapha kwakukulu kwa anthu, ndi ana anu awiri omwe Hofeni ndi Finehasi afa, ndipo likasa la Mulungu lalandidwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa