Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 5:4 - Buku Lopatulika

Ndipo mfumu ya Aejipito inanena nao, Inu, Mose ndi Aroni, chifukwa ninji mumasulira anthu ntchito zao? Mukani ku akatundu anu.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo mfumu ya Aejipito inanena nao, Inu, Mose ndi Aroni, chifukwa ninji mumasulira anthu ntchito zao? Mukani ku akatundu anu.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Koma mfumu ya ku Ejipito ija idafunsa Mose ndi Aroni kuti, “Chifukwa chiyani mukuŵasiyitsa ntchito yao Aisraele? Chokani apa, bwererani ku ntchito yanu.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Koma mfumu ya Igupto inati, “Mose ndi Aaroni, chifukwa chiyani mukuchititsa anthuwa kuti asagwire ntchito zawo? Bwererani ku ntchito zanu!”

Onani mutuwo



Eksodo 5:4
8 Mawu Ofanana  

Potero anawaikira akulu a misonkho kuti awasautse ndi akatundu ao. Ndipo anammangira Farao mizinda yosungiramo chuma, ndiyo Pitomu ndi Ramsesi.


Ndipo kunali masiku amenewo, atakula Mose, kuti anatulukira kukazonda abale ake, napenya akatundu ao; ndipo anaona munthu Mwejipito ali kukantha Muhebri, wa abale ake.


Ndamvanso kubuula kwa ana a Israele, amene Aejipito awayesa akapolo; ndipo ndakumbukira chipangano changa.


Ndipo akulu anati kwa mfumu, Munthu uyu aphedwetu; chifukwa analopetsa manja a anthu a nkhondo otsala m'mzinda muno, ndi manja a anthu onse, pakunena kwa iwo mau otero; pakuti munthu uyu safuna mtendere wa anthu awa, koma nsautso yao.


Pamenepo Amaziya wansembe wa ku Betele anatumiza kwa Yerobowamu mfumu ya Israele, ndi kuti, Amosi wapangira inu chiwembu pakati pa nyumba ya Israele; dziko silingathe kulola mau ake onse.


Ndipo anayamba kumnenera Iye, kuti, Tinapeza munthu uyu alikupandutsa anthu a mtundu wathu, ndi kuwaletsa kupereka msonkho kwa Kaisara, nadzinenera kuti Iye yekha ndiye Khristu mfumu.


Pakuti tapeza munthuyu ali ngati mliri, ndi woutsa mapanduko kwa Ayuda onse m'dziko lonse lokhalamo anthu, ndi mtsogoleri wa mpanduko wa Anazarene;