Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 23:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo anayamba kumnenera Iye, kuti, Tinapeza munthu uyu alikupandutsa anthu a mtundu wathu, ndi kuwaletsa kupereka msonkho kwa Kaisara, nadzinenera kuti Iye yekha ndiye Khristu mfumu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo anayamba kumnenera Iye, kuti, Tinapeza munthu uyu alikupandutsa anthu a mtundu wathu, ndi kuwaletsa kupereka msonkho kwa Kaisara, nadzinenera kuti Iye yekha ndiye Khristu mfumu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Iwo adayamba kuneneza Yesu kuti, “Munthu uyu tidampeza akusokeza anthu a mtundu wathu. Amatiletsa kuti tisamakhome msonkho kwa Mfumu ya ku Roma. Amanenanso kuti ati Iyeyu ndi Mpulumutsi wolonjezedwa uja ndiponso mfumu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Ndipo iwo anayamba kumuneneza nati, “Ife tinapeza munthu uyu akusokoneza anthu a mtundu wathu ndipo amatsutsa zopereka msonkho kwa Kaisara komanso amati ndi Khristu, Mfumu.”

Onani mutuwo Koperani




Luka 23:2
33 Mawu Ofanana  

Ndipo kunachitika pamene Ahabu anaona Eliya, Ahabu anati kwa iye, Kodi ndiwe uja umavuta Israeleyo?


Mboni za chiwawa ziuka, zindifunsa zosadziwa ine.


Komatu amkhalira upo kuti amkankhire pansi ulemu wake; akondwera nao mabodza; adalitsa ndi m'kamwa mwao, koma atemberera mumtima.


Pakuti ndamva kugogodera kwa ambiri, mantha pozungulira ponse. Neneza, ndipo tidzamneneza iye, ati atsamwali anga onse, amene ayang'anira kutsimphina kwanga; kapena adzakopedwa, ndipo ife tidzampambana iye, ndipo tidzambwezera chilango.


Ndipo akulu anati kwa mfumu, Munthu uyu aphedwetu; chifukwa analopetsa manja a anthu a nkhondo otsala m'mzinda muno, ndi manja a anthu onse, pakunena kwa iwo mau otero; pakuti munthu uyu safuna mtendere wa anthu awa, koma nsautso yao.


Pamenepo Amaziya wansembe wa ku Betele anatumiza kwa Yerobowamu mfumu ya Israele, ndi kuti, Amosi wapangira inu chiwembu pakati pa nyumba ya Israele; dziko silingathe kulola mau ake onse.


Ndipo ndinatha abusa atatuwo mwezi umodzi; pakuti mtima wanga unalema nao, ndi mtima waonso unaipidwa nane.


Koma kuti ife tisawakhumudwitse, pita iwe kunyanja, ukaponye mbedza, nuitole nsomba yoyamba kuwedza; ndipo ukaikanula pakamwa pake udzapezamo rupiya; tatenga limeneli, nuwapatse ilo pamutu pa iwe ndi Ine.


Nanena iwo, Cha Kaisara. Pomwepo Iye anati kwa iwo, Chifukwa chake patsani kwa Kaisara zake za Kaisara, ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.


Ndipo Yesu anaimirira pamaso pa kazembe, ndipo kazembeyo anamfunsa Iye kuti, Kodi Iwe ndiwe mfumu ya Ayuda? Ndipo Yesu anati kwa iye, Mwatero.


Ndipo Yesu anati kwa iwo, Perekani zake za Kaisara kwa Kaisara, ndi zake za Mulungu kwa Mulungu. Ndipo anazizwa naye kwambiri.


Ndipo Pilato anamfunsa Iye, Kodi ndiwe mfumu ya Ayuda? Ndipo anayankha, nanena naye, Mwatero.


nati kwa iwo, Munadza kwa ine ndi munthu uyu ngati munthu wakupandutsa anthu: ndipo taonani, Ine ndinamfunsa za mlanduwu pamaso panu, ndipo sindinapeze pa munthuyu chifukwa cha zinthu zimene mumnenera;


Koma iwo anapunda kunena kuti, Amautsa anthuwo, naphunzitsa mu Yudeya yense, kuyambira ku Galileya ndi kufikira kuno komwe.


Chifukwa chake Pilato anatulukira kunja kwa iwo, nati, Chifukwa chanji mwadza nacho cha munthu uyu?


Anayankha nati kwa iye, Akadakhala wosachita zoipa uyu sitikadampereka Iye kwa inu.


Pa ichi Pilato anafuna kumasula Iye; koma Ayuda anafuula, ndi kunena, Ngati mumasula ameneyo, simuli bwenzi la Kaisara; yense wodziyesera yekha mfumu atsutsana naye Kaisara.


Ndipo sangathe kukutsimikizirani zimene andinenera ine tsopano.


Pakuti tapeza munthuyu ali ngati mliri, ndi woutsa mapanduko kwa Ayuda onse m'dziko lonse lokhalamo anthu, ndi mtsogoleri wa mpanduko wa Anazarene;


Perekani kwa anthu onse mangawa ao; msonkho kwa eni ake a msonkho; kulipira kwa eni ake a kulipidwa; kuopa kwa eni ake a kuwaopa; ulemu kwa eni ake a ulemu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa