Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Amosi 7:10 - Buku Lopatulika

10 Pamenepo Amaziya wansembe wa ku Betele anatumiza kwa Yerobowamu mfumu ya Israele, ndi kuti, Amosi wapangira inu chiwembu pakati pa nyumba ya Israele; dziko silingathe kulola mau ake onse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Pamenepo Amaziya wansembe wa ku Betele anatumiza kwa Yerobowamu mfumu ya Israele, ndi kuti, Amosi wapangira inu chiwembu pakati pa nyumba ya Israele; dziko silikhoza kulola mau ake onse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Ku Betele kunali wansembe wina dzina lake Amaziya. Iyeyo adatumiza mthenga kwa Yerobowamu, mfumu ya ku Israele kuti, “Amosi akukuutsirani chiwembu pakati pa anthu a ku Israele. Anthu sangathe kuvomera zonse zimene iye akunenazo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Pamenepo Amaziya wansembe wa ku Beteli anatumiza uthenga kwa Yeroboamu mfumu ya Israeli kuti, “Amosi akukuutsirani chiwembu pakati pa Aisraeli. Dziko silingalekerere zonena zake zonsezo.

Onani mutuwo Koperani




Amosi 7:10
23 Mawu Ofanana  

Abale ake ndipo anati kwa iye, Kodi udzakhala mfumu yathu ndithu? Kapena udzatilamulira ife ndithu kodi? Ndipo anamuda iye koposa chifukwa cha maloto ake ndi mau ake.


Pambuyo pa ichi Yerobowamu sanabwerere panjira yake yoipa, koma analonganso anthu achabe akhale ansembe a misanje, yense wakufuna yemweyu anampatula akhale wansembe wa misanje.


Ndipo kunachitika pamene Ahabu anaona Eliya, Ahabu anati kwa iye, Kodi ndiwe uja umavuta Israeleyo?


Ndipo iwo anati, Tiyeni, tilingalire Yeremiya chomchitira choipa; pakuti chilamulo sichidzathera wansembe, kapena uphungu wanzeru, kapena mau mneneri. Tiyeni, timpande iye ndi lilime, tisamvere iye mau ake ali onse.


Ndipo panali, pamene anamva mau onse, anaopa nayang'anana wina ndi mnzake, nati kwa Baruki, Tidzamfotokozeratu mfumu mau awa onse.


Ndipo akulu anati kwa mfumu, Munthu uyu aphedwetu; chifukwa analopetsa manja a anthu a nkhondo otsala m'mzinda muno, ndi manja a anthu onse, pakunena kwa iwo mau otero; pakuti munthu uyu safuna mtendere wa anthu awa, koma nsautso yao.


Mau a Amosi, amene anali mwa oweta ng'ombe a ku Tekowa, ndiwo amene anawaona za Israele masiku a Uziya mfumu ya Yuda, ndi masiku a Yerobowamu mwana wa Yowasi mfumu ya Israele, zitatsala zaka ziwiri chisanafike chivomezi.


Pakuti tsiku lakumlanga Israele chifukwa cha zolakwa zake, ndidzalanganso maguwa a nsembe a ku Betele; ndi nyanga za guwa la nsembe zidzadulidwa, ndipo zidzagwa pansi.


Iwo adana naye wodzudzula kuchipata, nanyansidwa naye wolunjikitsa mau.


koma musamafuna Betele, kapena kumalowa mu Giligala; musamapita ku Beereseba; pakuti Giligala adzalowadi m'ndende, ndi Betele adzasanduka chabe.


Pakuti atero Amosi, Yerobowamu adzafa ndi lupanga, ndi Israele adzatengedwadi ndende, kuchoka m'dziko lake.


Ndipo m'mene Iye analowa mu Kachisi, ansembe aakulu ndi akulu a anthu anadza kwa Iye analikuphunzitsa, nanena, Muchita izi ndi ulamuliro wotani? Ndipo ndani anakupatsani ulamuliro wotere?


Ndipo anayamba kumnenera Iye, kuti, Tinapeza munthu uyu alikupandutsa anthu a mtundu wathu, ndi kuwaletsa kupereka msonkho kwa Kaisara, nadzinenera kuti Iye yekha ndiye Khristu mfumu.


Pakuti tapeza munthuyu ali ngati mliri, ndi woutsa mapanduko kwa Ayuda onse m'dziko lonse lokhalamo anthu, ndi mtsogoleri wa mpanduko wa Anazarene;


nanena, Tidakulamulirani chilamulire, musaphunzitsa kutchula dzina ili; ndipo taonani, mwadzaza Yerusalemu ndi chiphunzitso chanu, ndipo mufuna kutidzetsera ife mwazi wa munthu uja.


Koma pakumva izi analaswa mtima, namkukutira mano.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa