Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Amosi 7:11 - Buku Lopatulika

11 Pakuti atero Amosi, Yerobowamu adzafa ndi lupanga, ndi Israele adzatengedwadi ndende, kuchoka m'dziko lake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Pakuti atero Amosi, Yerobowamu adzafa ndi lupanga, ndi Israele adzatengedwadi ndende, kuchoka m'dziko lake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 “Amosiyo akunena kuti, ‘Yerobowamu adzafa pa nkhondo, ndipo Aisraele adzatengedwa kunka ku ukapolo, kutali ndi dziko lao.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Pakuti zimene Amosi akunena ndi izi: “ ‘Yeroboamu adzaphedwa ndi lupanga, ndipo Israeli adzapita ndithu ku ukapolo, kutali ndi dziko lake.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Amosi 7:11
13 Mawu Ofanana  

Chaka chachisanu ndi chinai cha Hoseya mfumu ya Asiriya analanda Samariya, natenga Aisraele andende, kunka nao ku Asiriya; nawakhalitsa mu Hala, ndi mu Habori, ku mtsinje wa Gozani, ndi m'mizinda ya Amedi.


Tsiku lonse atenderuza mau anga, zolingirira zao zonse zili pa ine kundichitira choipa.


Bwanji mwanenera m'dzina la Yehova, kuti, Nyumba iyi idzafanana ndi Silo, mzinda uwu udzakhala bwinja lopanda wokhalamo? Ndipo anthu onse anamsonkhanira Yeremiya m'nyumba ya Yehova.


Ndipo panali, pamene anamva mau onse, anaopa nayang'anana wina ndi mnzake, nati kwa Baruki, Tidzamfotokozeratu mfumu mau awa onse.


Mau a Amosi, amene anali mwa oweta ng'ombe a ku Tekowa, ndiwo amene anawaona za Israele masiku a Uziya mfumu ya Yuda, ndi masiku a Yerobowamu mwana wa Yowasi mfumu ya Israele, zitatsala zaka ziwiri chisanafike chivomezi.


Pamenepo Amaziya wansembe wa ku Betele anatumiza kwa Yerobowamu mfumu ya Israele, ndi kuti, Amosi wapangira inu chiwembu pakati pa nyumba ya Israele; dziko silingathe kulola mau ake onse.


Amaziya anatinso kwa Amosi, Mlauli iwe, choka, thawira kudziko la Yuda, nudye, nunenere komweko;


ndi misanje ya Isaki idzakhala bwinja; ndi malo opatulika a Israele adzapasuka; ndipo ndidzaukira nyumba ya Yerobowamu ndi lupanga.


Udziyeseze wadazi, udzimete wekha chifukwa cha ana ako okondwera nao; kuza dazi lako ngati la muimba; pakuti anakuchokera, nalowa ndende.


nati, Uyu ananena kuti, Ndikhoza kupasula Kachisi wa Mulunguyu, ndi kummanganso masiku atatu.


pakuti tinamumva iye alikunena, kuti, Yesu Mnazarayo amene adzaononga malo ano, nadzasanduliza miyambo imene Mose anatipatsa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa