Nalichotsa guwa la nsembe lamkuwa linali pamaso pa Yehova, nalichotsa ku khomo la nyumba pakati paguwa lake la nsembe ndi nyumba ya Yehova, naliika kumpoto kwa guwa lake la nsembe.
Eksodo 40:6 - Buku Lopatulika Ndipo ukaike guwa la nsembe yopsereza kunja kwa khomo la Kachisi wa chihema chokomanako. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ukaike guwa la nsembe yopsereza kunja kwa khomo la Kachisi wa chihema chokomanako. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Uike guwa lootcherapo nsembe patsogolo pa chihema chamsonkhanocho. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Uyike guwa lansembe yopsereza patsogolo pa chipata cha chihema, tenti ya msonkhano. |
Nalichotsa guwa la nsembe lamkuwa linali pamaso pa Yehova, nalichotsa ku khomo la nyumba pakati paguwa lake la nsembe ndi nyumba ya Yehova, naliika kumpoto kwa guwa lake la nsembe.
Ndipo anaika guwa la nsembe yopsereza pa khomo la Kachisi wa chihema chokomanako, natenthapo nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa; monga Yehova adamuuza Mose.
Ndipo ukaike guwa la nsembe lofukizapo lagolide chakuno cha likasa la mboni, numange pa chihema nsalu yotsekera pakhomo.
Ukaikenso mkhate pakati pa chihema chokomanako, ndi guwa la nsembe, ndi kuthiramo madzi.
Pamenepo aiphe ng'ombeyo pamaso pa Yehova; ndipo ana a Aroni, ansembewo, abwere nao mwazi, nawaze mwaziwo pozungulira paguwa la nsembe, lokhala pa khoma la chihema chokomanako.
ndipo Iye ndiye chiombolo cha machimo athu; koma wosati athu okha, komanso a dziko lonse lapansi.