Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Levitiko 1:5 - Buku Lopatulika

5 Pamenepo aiphe ng'ombeyo pamaso pa Yehova; ndipo ana a Aroni, ansembewo, abwere nao mwazi, nawaze mwaziwo pozungulira paguwa la nsembe, lokhala pa khoma la chihema chokomanako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Pamenepo aiphe ng'ombeyo pamaso pa Yehova; ndipo ana a Aroni, ansembewo, abwere nao mwazi, nawaze mwaziwo pozungulira pa guwa la nsembe, lokhala pa khoma la chihema chokomanako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Pambuyo pake aiphe pamaso pa Chauta, ndipo ansembe, ana a Aroni, abwere ndi magazi ake. Awaze magaziwo mozungulira guwa limene lili pa khomo la chihema chamsonkhano.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Pambuyo pake aphe ngʼombeyo pamaso pa Yehova, ndipo ansembe, ana a Aaroni, atenge magazi ake ndi kuwawaza mbali zonse za guwa lansembe limene lili pa khomo la tenti ya msonkhano.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 1:5
25 Mawu Ofanana  

Pamenepo anaphera Paska; ndi ansembe anawaza mwazi adaulandira m'manja mwa Alevi amene anasenda nsembezo.


Nuphe ng'ombe yamphongoyo pamaso pa Yehova, pa khomo la chihema chokomanako.


Nuiphe nkhosa yamphongoyo, ndi kutenga mwazi wake, ndi kuuwaza paguwa la nsembe pozungulira.


Ndipo ukaike guwa la nsembe yopsereza kunja kwa khomo la Kachisi wa chihema chokomanako.


momwemonso Iye adzawazawaza mitundu yambiri; mafumu adzamtsekera Iye pakamwa pao; pakuti chimene sichinauzidwe kwa iwo adzachiona, ndi chimene iwo sanamve adzazindikira.


Ndipo ndidzakuwazani madzi oyera, ndipo mudzakhala oyera; ndidzakuyeretsani kukuchotserani zodetsa zanu zonse, ndi mafano anu nonse.


Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, atero Ambuye Yehova, Malemba a guwa la nsembe, tsiku lakulimanga, kuperekapo nsembe zopsereza, ndi kuwazapo mwazi, ndi awa;


Ndipo aiphere iyo pa mbali ya kumpoto ya guwa la nsembe, pamaso pa Yehova; ndipo ana a Aroni, ansembewo, awaze mwazi wake paguwa la nsembe pozungulira.


Ndipo wansembe abwere nacho ku guwa la nsembe, namwetule mutu wake, naitenthe paguwa la nsembe; ndi mwazi wake aukamulire pa mbali ya guwa la nsembe,


Pamenepo aiphe mbuzi ya nsembe yauchimo, ndiyo yophera anthu, nalowe nao mwazi wake m'tseri mwa nsalu yotchinga, nachite nao mwazi wake monga umo anachitira ndi mwazi wa ng'ombe, nauwaze pachotetezerapo ndi chakuno cha chotetezerapo;


Pakuti moyo wa nyama ukhala m'mwazi; ndipo ndakupatsani uwu paguwa la nsembe, uchite chotetezera moyo wanu; pakuti wochita chotetezera ndiwo mwazi, chifukwa cha moyo wake.


naike dzanja lake pamutu pake, naiphe pa khomo la chihema chokomanako; ndipo ana a Aroni awaze mwazi wake paguwa la nsembe pozungulira.


Ndipo aike dzanja lake pamutu wa chopereka chake, ndi kuipha pa chipata cha chihema chokomanako; ndipo ana a Aroni, ansembewo, awaze mwazi wake paguwa la nsembe pozungulira.


naike dzanja lake pamutu pa chopereka chake, naiphe patsogolo pa chihema chokomanako; ndipo ana a Aroni awaze mwazi wake paguwa la nsembe pozungulira.


Aike dzanja lake pamutu pa nsembe yauchimo, naiphe nsembe yauchimo pamalo pa nsembe yopsereza.


Naike dzanja lake pamutu wa nsembe yauchimo, ndi kuipha ikhale nsembe yauchimo pamalo pophera nsembe yopsereza.


Ndipo wansembeyo atengeko mwazi, nauike pa nyanga za guwa la nsembe la chofukiza cha fungo lokoma, lokhala m'chihema chokomanako pamaso pa Yehova; nathire mwazi wonse wa ng'ombeyo patsinde paguwa la nsembe yopsereza, lokhala pa khomo la chihema chokomanako.


Ndidzafika kwa Yehova ndi chinai, ndi kuwerama kwa Mulungu Wam'mwamba? Kodi ndifike kwa Iye ndi nsembe zopsereza, ndi anaang'ombe a chaka chimodzi?


Koma ng'ombe yoyamba kubadwa, kapena nkhosa yoyamba kubadwa, kapena mbuzi yoyamba kubadwa, usaziombola; ndizo zopatulika; uwaze mwazi wake paguwa la nsembe, ndi kufukiza mafuta ao, nsembe yamoto ya fungo lokoma kwa Yehova.


Ndipotu wansembe aliyense amaima tsiku ndi tsiku, natumikira, napereka nsembe zomwezi kawirikawiri, zimene sizingathe konse kuchotsa machimo;


ndi kwa Yesu Nkhoswe ya chipangano chatsopano, ndi kwa mwazi wa kuwaza wakulankhula chokoma choposa mwazi wa Abele.


monga mwa kudziwiratu kwa Mulungu Atate, m'chiyeretso cha Mzimu, chochitira chimvero, ndi kuwaza kwa mwazi wa Yesu Khristu: Chisomo, ndi mtendere zichulukire inu.


Ndipo iwo anapha ng'ombe, nabwera naye mwanayo kwa Eli.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa