Ndipo uuze ana a Israele akutengere mafuta a azitona oyera opera akuunikira, kuti awalitse nyali kosalekeza.
Eksodo 40:4 - Buku Lopatulika Ulongenso gomelo, nukonzerepo zokonzera zake; ulongenso choikaponyalicho, ndi kuyatsa nyali zake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ulongenso gomelo, nukonzerepo zokonzera zake; ulongenso choikapo nyalicho, ndi kuyatsa nyali zake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ukhazikemonso tebulo, pamwamba pake uikepo zipangizo zake, ndipo uikemo choikaponyale ndi nyale zake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ulowetsemo tebulo ndi kuyika zimene zimakhala pamenepo. Kenaka ulowetse choyikapo nyale ndipo uyikepo nyale zake. |
Ndipo uuze ana a Israele akutengere mafuta a azitona oyera opera akuunikira, kuti awalitse nyali kosalekeza.
Nthawi zonse tsiku la Sabata aukonze pamaso pa Yehova, chifukwa cha ana a Israele, ndilo pangano losatha.