Levitiko 24:8 - Buku Lopatulika8 Nthawi zonse tsiku la Sabata aukonze pamaso pa Yehova, chifukwa cha ana a Israele, ndilo pangano losatha. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20148 Nthawi zonse tsiku la Sabata aukonze pamaso pa Yehova, chifukwa cha ana a Israele, ndilo pangano losatha. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa8 Pa tsiku la Sabata lililonse Aroni aziika makeke a nsembeyo mosalephera pamaso pa Chauta m'malo mwa Aisraele, kuti chikhale chipangano chamuyaya. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero8 Sabata ndi sabata nthawi zonse Aaroni aziyika makeke amenewa pamaso pa Yehova mʼmalo mwa Aisraeli onse kuti akhale pangano lamuyaya. Onani mutuwo |
Taonani, nditi ndilimangire dzina la Yehova Mulungu wanga nyumba, kumpatulira iyo, ndi kufukiza pamaso pake zonunkhira za fungo lokoma, ndiyo ya mkate woonekera wachikhalire, ndi ya nsembe zopsereza, m'mawa ndi madzulo, pamasabata, ndi pokhala mwezi, ndi pa zikondwerero zoikika za Yehova Mulungu wathu. Ndiwo machitidwe osatha mu Israele.